Matayo 5
5
Yesu waayaluza wandhu kuphili
1Yesu yapo wadayaona magulu ya wandhu wadakwela kuphili. Ndiipo wadakhala panjhi. Woyaluzidwa wake adamchata. 2Nayo wadayamba kwaayaluza,
Chikondwelo cha zene
Luka 6:20-23
3“Ali ni mwawi wajha ajhiwa kuti amfuna Mnungu
pakuti ufumu wa kumwamba ni wao.”
4“Ali ni mwawi yao ali ni chisoni
pakuti siathilidwe mtima.”
5“Ali ni mwawi yao ajhichicha
pakuti Mnungu siwapache jhiko likhale lao.”
6“Ali ni mwawi yao afuna kupunda kuchita ivo vimkwadilicha Mnungu
ndande Mnungu siwatangatile kuchita chimwecho.”
7“Ali ni mwawi wajha alengela wina lisungu
pakuti Mnungu siwalengele lisungu.”
8“Ali ni mwawi yao ali ni mtima wabwino
pakuti saamuone Mnungu.”
9“Ali ni mwawi wajha apeleka mtendele
pakuti siatanidwe wana a Mnungu.”
10“Ali ni mwayi anyiyao avutichidwa ndande ya kuchita yayo wafuna Mnungu
Pakuti ufumu wa kumwamba ni wao!”
11“Muli ni mwawi wandhu yapo sakutukwaneni ni kukuvutichani ni kukunamizilani voipa ndande yanga. 12Kondwani ni lulutilani pakuti chikho chanu chachikulu chaikidwa kumwamba. Mchimwecho nde umo adaavuticha alosi akhale anyiimwe mkali wosabdwa.”
Mchele wa chinyope ni dangalila
Maluko 9:50; Luka 14:34-35
13“Anyiimwe ni mchele wa chinyope wa jhiko. Nambho mchele wa chinyopeo ngati wasukuluka sikomelechedwe ni chiyani? Ulibe njhito. Siutaidwe kubwalo nikupondedwa ni wandhu.”
14“Anyiimwe ni dangalila la jhiko! Ni ngati nyumba iyo yamangidwa pamwamba pa phili siukhoza kubisika. 15Wandhu saakweleza nyali ni kuikupika kwa debe. Nambho iyikidwa pamwamba poikila nyali kuti imulikile wandhu wonjhe yao ali mnyumba. 16Chimwecho dangalila lanu liwale pamaso pa wandhu kuti apenye vichito vanu vabwino ni kwaakweza Atate wanu akumwamba.”
Yesu wayaluza wandhu thauko
17“Msadaganiza kuti najha kuchocha thauko la Musa ilo wadapachidwa ni Mnungu ni mayaluzo ya alosi. Sinidajhe kuchocha nambho najha kukufotokozelani kuti mayaluzo yameneyo ni yazene. 18Zene nikukambilani palibe ata kandhu kamojhi kakang'ono kupunda yako sikachochedwe mu thauko mbaka yonjhe yapo siyakwanile. 19Waliyonjhe uyo siwachata thauko laling'ono kuchokela mthauko ili nikwaayaluza wina kuti achite chimwecho. Mmeneyo siwakhale womng'ono kupunda mu ufumu wa kumwamba. Nambho yujha wachata thauko ni kwaayaluza wina, mmeneyo siwakhale wamkulu mu ufumu wa kumwamba. 20Zene nikukambilani ngati simuchita umo wafunila Mnungu kupitilila umo achitila Afalisayo ni oyaluza a thauko simulowa mu ufumu wa kumwamba ata pang'ono.”
Mayaluzo kuusu kukwiya
Luka 12:57-59
21“Mwavela umo adakambilidwa wandhu a kale, ‘Simudapha!’ Ni mundhu waliyonjhe uyo siwaphe siwalamulidwe. 22Nambho ine nikukambilani waliyonjhe wamkwiyila mbale wake lazima walamulidwe. Uyo wampepula mbale wake nikuona walibe mate siwapelekedwe kunyumba ya milandu. Uyo wamtana mbale wake, ‘Sabobwa,’ wali pafupi kulowa mu moto wa ku jehanamu. 23Ngati umchochela Mnungu njhembe yopyeleza pa guwa ni ukakumbukila kuti wayambana ni mbale wako, 24isiye njhembe yako pachogolo pa guwa. Pita uti ukavane ni mbale wako. Ndiipo ubwele umchochele Mnungu njhembe yako yopyeleza.”
25“Vana ni uyo wakupeleka kunyumba yamilandu mkali mnjila. Popande chimwecho uyo wakushitaki siwakupeleke kwa mlamuli wa nyumba ya milandu. Nayo mlamuli siwakupeleke kwa asikali. Nayo siwakuike mndende. 26Zene nikukambilani simuchoka mmenemo mbaka mlipe ndalama yonjhe iyo udaidwa.”
Mayaluzo kuusu chigololo
27Yesu wadaendekela kukamba, “Mwavela kuti wandhu adakambilidwa, ‘Usadachita chigololo!’ 28Nambho ine nikukambilani kuti uyo siwampenye wamkazi kwa kumkhumbila wathochita chigololo mumtima mwake. 29Ngati diso lako la kwene likakuchiticha kuti uchite chimo lizule ni kulitaya kutali. Mbasa kutaiza chiwalo chimojhi cha thupi lako kusiyana ni thupi lako lonjhe kutaidwa ku jehanamu ya moto. 30Ngati jhanja lako la kwene likuchiticha kuti uchite chimo lidule ni ukalitaye kutali ni iwe. Mbasa kutaiza chiwalo chimojhi cha thupi lako kusiyana ni thupi lako lonjhe kutaidwa ku jehanamu ya moto.”
Nghani za talaka
Matayo 19:9; Maluko 10:11-12; Luka 16:18
31“Idathokambidwanjho, ‘Mundhu waliyonjhe wakafuna kumleka mkazake ifunika wampache talaka.’ 32Nambho ine nikukambilani mundhu waliyonjhe uyo siwamsiye mkazake kwa ndande yaliyonjhe ijha ni osati kwa ndande ya chigololo wamchita mkazake kukhala wachigololo, ni wammuna waliyonjhe uyo siwamkwate wamkazi uyo wasiidwa nayo wachita chigololo.”
Nghani ya chilanga
33“Mwavelanjho kuti wandhu akale adakambidwa, ‘Usadasiya kuchita icho udaahidi, nambho ufunika kuchita ahadi zonjhe udaahidi kwa Ambuye.’ 34Nambho ine nikukambilani msadalumbila chilanga chilichonjhe yapo muahidi. Ni msadalumbila kwa mwamba pakuti umenewo ni mpando wa chifumu wa Mnungu. 35Chinchijha msadalumbila kwa jhiko pakuti ni malo yake yoikila miyendo. Ni msadalumbila kwa jhiko la Yelusalemu pakuti umenewo nde mujhi wa Mfumu wamkulu. 36Usadalumbilanjho kwa mutu pakuti siukhoza kuchita ata chichi limojhi kukhala lakuda kapina loyela. 37Ukakamba, ‘Yetu’ basi ikhale ‘Yetu.’ Ukakamba, ‘Notho’ basi ikhale ‘Notho.’ Chalichonjhe icho chipitilila nghani zimenezo chichoka kwa Woyesa.”
Nghani yobwezela mbwezo
Luka 6:29-30
38“Mwavela kuti idakambidwa, ‘Diso kwa diso ni jhino kwa jhino.’ 39Nambho ine nikukambilani, msadabwezela mbwezo kwa mundhu uyo wakuchitila voipa. Mundhu wakakubula mbama kuchakaya la kwene chinchijha mleke wakubule chakaya lakawili. 40Ngati mundhu wakafuna kukupeleka kubwalo la milandu ni kufuna kutenga laya lako msiye watenge ni khoti lako. 41Ngati mundhu wakakukamiza kutenga katundu wake kilo meta imojhi mpelekele kwa kilometa ziwili. 42Mundhu uyo wakupembha kandhu mpache. Uyo wafuna kukukongola usadammana.”
Kwakonda adani
Luka 6:27-28,32-36
43“Mwavela kuti idakambidwa kuti, ‘Mkonde mnjako ni umuipile mdani wako.’ 44Nambho ine nikukambilani akondeni adani wanu ni kwapembhela anyiyao akuvutichani anyiimwe, 45kuti mkhale wana wa Atate wanu ali kumwamba. Pakuti iye wawalichila jhuwa lake wandhu woipa ni wandhu abwino ni kwanyechela vula wandhu yawo achita ivo vivomelezeka kwa Mnungu ni wandhu yawo saachita vovomelezeka. 46Bwanji, simupate chikho chanji ngati simwaakonde wajha akukondanipe? Palibe! Pakuti olandila malipilo nawo achita chimwecho. 47Chinchijha ngati mkaalonjela abale wanupe bwanji, mchita chindhu chanji chachikulu kupitilila wandhu wina? Ata wandhu yawo samjhiwa Mnungu saachita chimwecho. 48Chimwecho khalani wokwanila ngati Tate wanu wa kumwamba umo wali okwanila.”
Actualmente seleccionado:
Matayo 5: NTNYBL2025
Destacar
Compartir
Copiar

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.