Logo de YouVersion
Icono de búsqueda

Matayo 4

4
Yesu wayesedwa
Maluko 1:12-13; Luka 4:1-13
1Ndiipo Mzimu Woyela udamchogoza Yesu mbaka kuphululu kuti waesedwe ni Satana. 2Yesu wadamanga masiku alubaini usiku ni usana ndiipo wadavela njala. 3Ndiipo woyesa wadamchata, Wadamkambila, “Ikakhala iwe Mwana wa Mnungu, Lamula myala iyi ikhale mabumunda.”
4Yesu wadamuyangha, “Yalembedwa, ‘Mundhu siwakhala wa moyo kwa bumundape, Nambho kwa kila malembo yoyela yakambidwa ni Mnungu.’”
5Ndiipo Woyesa wadamtenga Yesu mbaka ku Yelusalemu mujhi woyela. Wadamkweza mbaka pamwamba kupunda pa chindupa la nyumba ya Mnungu. 6Wadamkambila, “Ngati iwe ni Mwana wa Mnungu jhitaye panjhi. Pakuti yalembedwa,
‘Mnungu siwakutumile atumiki wake akumwamba
saakutenge mmanja mwao
kuti siudajhikhuwala mwendo wako pa mwala.’”
7Yesu wadayangha, “Chinchijha yalembedwa, ‘Usadamuyesa Ambuye Mnungu wako.’”
8Ndiipo Woyesa wadamtenganjho Yesu mbaka pa mwamba pa phili la litali. Wadamlangiza ufumu wonjhe wa jhiko ni ufulu wajhiko. 9Wadamkambila, “Vindhu vonjhevi sinikupache ngati siunigwadile ni kunilambila.”
10Yesu wadamkambila, “Chokapo yapa iwe Woyesa! Yalembedwa mmalembo ya Mnungu, ‘Waalambile Ambuye Mnungu wako ni kwaatumikila iwo okha.’”
11Ndiipo Woyesa wadamleka Yesu ni atumiki a kumwamba adajha kumtumikila.
Yesu wayamba njhito yake kumujhi wa Galilaya
Maluko 1:14-15; Luka 4:14-15
12Yesu yapo wadavela kuti Yohana waikidwa mndende wadapita kumujhi wa Galilaya. 13Wadachoka ku Nazaleti wadapita kukhala kumujhi wa Kapelinaumu mujhi uli pafupi ni nyanja ya Galilaya mumalile ya mayiko ya Zabuloni ni Nafutali. 14Chindhu ichi chidachitika kuti chikwanile chijha chidakambidwa ni mlosi Isaya,
15“Jhiko la Zebuloni ni jhiko la Nafutali
kunjila ipita mnyanja kuchijya la mchinje Yolodani,
Mgalilaya mjhiko ilo akhala wandhu yawo osati Ayahudi!
16Wandhu yawo adakhala mumdima aliona dangalila lalikulu.
Wandhu yawo amakhala mujhiko la mchitunjhi cha nyifa dangalila lawalila.”
17Kuchokela nyengo imeneyo Yesu wadayamba kulalikila niwakamba, “Siyani kuchita machimo pakuti ufumu wa kumwamba wawandikila!”
Yesu waatana alovi anayi
Maluko 1:16-20; Luka 5:1-11
18Yesu yapo wamaenda mphepete mwa nyanja ya Galilaya wadaona abale awili, Simoni uyo wamatanidwa Petulo ni Anduleya. Amavuwa njhomba mnyanja kwa makoka yawo. 19Yesu wadaakambila, “Majhani nichateni! Nane sinikuchiteni mukhale opeleka wandhu kwa Mnungu.” 20Pampajha adayasiya makoka yao niadamchata.
21Yapo wadapita pachogolo wadaaona abale wina awili, Yakobo ni Yohana wana a Zebedayo. Anyiiwo adali mkati mwa boti pamojhi ni atatewao a Zebedayo amatambasula makoka yao. Yesu wadaatana. 22Pampajha adalisiya boti ni atate wao ni kumchata Yesu.
Yesu wayaluza ni kwaalamicha wandhu
Luka 6:17-19
23Yesu wadaendela malo yonjhe ya Galilaya. Wadayaluza mnyumba yokomanilana Ayahudi ni wadalalikila uthenga wa Ufumu wa Mnungu. Wadalamicha kila mtundu wa matenda ni mavuto yonjhe. 24Nghani zake zidayenela madela yonjhe ya Siliya. Chimwecho wandhu adaampelekela wodwala wonjhe ni anyiyawo amavutika ni kila mtundu wa matenda ni ozamwa ni viwanda ni anjilinjili ni ovulala. Nayo wadalamicha wonjhe. 25Magulu yambili ya wandhu kuchokela mujhiko la Galilaya ni Dekapoli ni Yelusalemu ni Yudea ni chijya la mchinje Yolodani yadamchata Yesu.

Actualmente seleccionado:

Matayo 4: NTNYBL2025

Destacar

Compartir

Copiar

None

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión