Hoseya 3
3
Hoseya Ayanjana ndi Mkazi Wake
1Yehova anati kwa ine, “Pita kamukondenso mkazi wako, ngakhale ali pa chibwenzi ndi wina ndi kuti ndi wachigololo. Mukonde iyeyo monga momwe Yehova amakondera Aisraeli, ngakhale iwo amapita kukapembedza milungu ina ndi kukonda nsembe za keke zamphesa zowuma.”
2Motero ndinamukwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iwiri ya barele. 3Kenaka ndinamuwuza mkaziyo kuti, “Ukhale nane masiku ambiri; usachitenso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina, ndipo ine ndidzakhala nawe.”
4Pakuti Aisraeli adzakhala masiku ambiri opanda mfumu kapena kalonga, osapereka nsembe kapena kuyimika miyala yachipembedzo, wopanda efodi kapena fano. 5Pambuyo pake Aisraeli adzabwerera ndi kufunafuna Yehova Mulungu wawo ndi Davide mfumu yawo. Adzabwera kwa Yehova akunjenjemera ndipo adzalandira madalitso mʼmasiku awo otsiriza.
S'ha seleccionat:
Hoseya 3: CCL
Subratllat
Copia
Compara
Comparteix
Vols que els teus subratllats es desin a tots els teus dispositius? Registra't o inicia sessió
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.