Maluko 13
13
Yesu wakamba nghani za kugomoledwa kwa nyumba ya Mnungu.
Matayo 24:1-2; Luka 21:5-6
1Yesu yapo wamachoka kubwalo kwa kunyumba ya Mnungu, oyaluzidwa wake mmohji wadamkambila, “Oyaluza, penyani myala iyi ni nyumba izi umo zakadwila!” 2Yesu wadamuyangha, “Bwanji, uzizizwa nyumba izi umo zakulila? Palibe ata mwala umojhi uwo siukhalile pamwamba pa wina, kila mwala siugomoledwe.”
Kulaga ni kuvutika
Matayo 24:3-14; Luka 21:7-19
3Yesu yapo wadakhala pamwamba pa phili la Mizeituni, kuchijya la Nyumba ya Mnungu, pamenepo Petulo ni Yakobo ni Yohana ni Andulea adamfunjha yapo adali pawokha, 4“Mtikambile vindhu vimenevo sivichokele siku lanji? Ni chizindikilo chanji icho sichilangize kuti vindhu vimenevo vili pafupi kujha?”
5Yesu wadayamba kwakambila, “Mkhalemaso mundhu waliyonjhe siwadakunyengani. 6Wandhu ambili siajhe niatumila jhina langa, nikukamba mthila, ‘Ine nde Kilisito.’ Ni siwaanyenge wandhu ambili. 7Yapo simvele nghani za nghondo, ni mbili za nghondo, simudaopa. Vindhu vimenevo lazima vichokele, nambho mathelo yakali siyadafike. 8Wandhu ajhiko limojhi siabulane ni wandhu ajhiko lina, ufumu umojhi siubulane ni ufumu wina, kumalo kwambili sikukhale ni chimtingiza cha ndhaka ni njala yaikulu. Yaya yonjhe siyakhale ngati chiyambo cha uchungu wa kujhimasula mwana.”
9“Nambho anyiimwe mkhale maso. Pakuti wandhu saakugwileni ni kukupelekani ku bwalo la milandu. Saakubuleni ku nyumba zokomanilana Ayahudi. Simpelekedwe kwa alamuli ni mafumu ndande ya ine, kuti mwalalikile Uthenga Wabwino. 10Mathelo yakali osafike, Uthenga Wabwino ufunika ulalikidwe mmayiko yonjhe. 11Yapo siakugwileni ni kukupelekani ku bwalo la milandu, msadaganizila chokamba. Ndhawi ikajha kambani chalinjhonjhe icho simpachidwe, pakuti osati anyiimwe simkambe nambho Mzimu Woyela. 12Ndhawi imeneyo mbale siwamchoche mbale wake wapedwe, ni tate siwamchoche mwana wake wapedwe, wana nao ni siabula obala wao ni kuwapha. 13Wandhu wonjhe siakuipileni anyiimwe ndande munichata ine. Nambho uyo siwalimbe mtima mpaka potela nde uyo siwaomboledwe.”
Mavuto yayakulu siyajhe
Matayo 24:15-28; Luka 21:20-24
14“Yapo simuone, Chindhu cha kumdingha Mnungu, chili munyumba ya Mnungu, pamenepo, anyiawo ali ku jhiko la Yudea athawile kuphili, mundhu uyo wasoma wajhiwe mate yake. 15Mundhu waliyonjhe uyo wali kubwalo kwa nyumba yake siwadalowa mkati kutenga chindhu chilichonjhe. 16Mundhu uyo wali kumunda siwadabwela kukhomo kutenga njhalu yake. 17Savutike kupunda anyamaye yawo ali ni pathupi ni oyamwicha siku zimenezo! 18Apembheni a Mnungu kuti vindhu vimenevo sividachokela nyengo yozizila. 19Siku zimenezo sikukhale ni mavuto yayo siyadachokelepo kuyambila yapo Mnungu wadaumba jhiko mbaka chipano, ni siyachokelanjho. 20Ngati Ambuye siadakazichepecha siku zimenezo palibe mundhu uyo wadakalama. Nambho ndande ya wandhu wake wasangha, Ambuye siazichepeche siku zimenezo.”
21“Pa masiku yameneyo mundhu waliyonjhe wakakumbilani, ‘Kilisito Muomboli wali pano,’ kapina, ‘Wali yapo,’ simdakhulupilila. 22Pakuti siachokele Alosi amthila ni wandhu ajhitana, ‘Ine ni Kilisito!’ Siachite vizindikilo ni vodabwicha, kuti ngati ikakhozekana anyenge wandhu asanghidwa ni Mnungu. 23Khalani maso! Ine nakukambilani kila chindhu icho sichichokele.”
Mwana wa Mundhu siwajhe
Matayo 24:29-31; Luka 21:25-28
24“Ndiipo, siku zimenezo, yapo siyathe mavuto yameneyo, jhuwa silikhale mdima ni mwezi siuchocha dangalila. 25Ndhondwa sizigwe kuchokela kumlengalenga, ni vindhu ivo vili kumlengalenga sivitingizidwe. 26Pamenepo wandhu sianione ine Mwana wa Mundhu, ninijha nili mmitambo kwa mbhavu zambili ni ulemelelo. 27Ndiipo sinaatume atumiki akumwamba wakuse wandhu wanga nidaasangha kuchokela kumadela yonjhe yanayi ya jhiko, kuchokela mmathelo ya jhiko, mbaka mmathelo ya kumwamba.”
Yaluzo la mtengo wa mtini
Matayo 24:32-35; Luka 21:29-33
28“Jhiyaluzeni chifani ichi kuchokela kwa mtengo wa mtini, ndhawi zake yapo ziyamba kuphukila ni kuchocha machamba, mjhiwa kuti nyengo ya mwavu yawandikila. 29Chinchijha yapo simuone vindhu ivo nidakukambilani ni vichokela, jhiwani kuti ine mwana wa Mundhu niwandikila kujha. 30Nikukambilani uzene, wandhu a mbadwa uwu siumwalila mbaka yaya yonjhe yachokele. 31Kumwamba ni jhiko sivimwalile, nambho mawuyanga siyakhale muyaya.”
Palibe uyu wajhiwa siku wala ndhawi
Matayo 24:36-44
32“Palibe mundhu waliyonjhe wajhiwa, siku kapina ndhawi imeneyo ata atumiki akumwamba kapina ine mwana wa Mnungu, nambho Mnungu yokha, nde uyo wajhiwa. 33Mkhale maso ni mchezelele, ndande simjhiwa wabwela ndhawi yanji. 34Ilingana ni mundhu uyo wadachoka ni kupita kuulendo, kwasiila akapolo wake alonde kila chindhu, kila mundhu wadampacha njhito yake yopota. Ni wadamlamula mlonda wa pakhomo wakhale maso. 35Chimwecho mchezelele, pakuti simjhiwa liti mwene nyumba siwabwele, siwabwele ujhulo, kapina usiku pakati kapina tambala yapo siwalile, kapina umawa. 36Wakabwela kwa chizulumukila siwadakupezani mwagona. 37Ichi nikukambilani anyiimwe, chimchijha naakambila wandhu wonjhe. Mkhale maso!”
Àwon tá yàn lọ́wọ́lọ́wọ́ báyìí:
Maluko 13: NTNYBL2025
Ìsàmì-sí
Pín
Daako
Ṣé o fẹ́ fi àwọn ohun pàtàkì pamọ́ sórí gbogbo àwọn ẹ̀rọ rẹ? Wọlé pẹ̀lú àkántì tuntun tàbí wọlé pẹ̀lú àkántì tí tẹ́lẹ̀
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.