Maluko 12
12
Yesu walinganicha achogoleli wa Ayahudi ni alimi akupha
Matayo 21:33-46; Luka 20:9-19
1Yesu wadayamba kukamba nawo kwa vifani, “Mundhu mmojhi wadavyala mizabibu mmunda. Ndiipo wadazingizila seli, ni pakati pake wadakonja malo yo finyila zabibu ni kumanga chilindo. Wadabwelekecha munda umeneo kwa alimi, wadachoka ni kupita kujhiko la kutali. 2Nyengo yokolola zabibu yapo idafika, wadaatuma kapolo wake kwa anyiwajha alimi, kuti akamtengele zabibu kuchoka mmunda mwake. 3Anyiwajha alimi adamgwila ni kumbula, ni adamtopola manja ya chajhe. 4Yujha mwene munda wadamtumanjho kapolo mwina, nayo adambula kumutu ni kumchitila vindhu voipa. 5Yujha mwene munda wadamtumanjho akapolo mwina, ni anyiwanjha alimi adampha. Mwene munda wadaatumanjho akapolo wina ambili, akapolo akumojhi adaabula ni akapolo akumojhi adaphedwa. 6Wadakhalila ni mundhu mmojhipe, wakumtuma mmeneyo nde mwanawake, uyo wamamkonda kupunda. Wadamtuma uku ni wakamba, ‘Uyu siamvechele ndande mwanawanga.’ 7Nambho anyiwajha alimi adakambilana, ‘Uyu nde mlisi wa munda uno, chipano, timuphe kuti munda uwu ukhale wathu!’ 8Chimwecho, adamgwila ni kumpha ni kumtaila kubwalo kwa ujha munda wa mizabibu.”
9Yesu wadaafunjha, “Bwanji, mwene munda siwachite chiyani? Siwajhe kuwapha alimi ameneo wonjhe ni kuubwelekecha munda umeneo wa mizabibu kwa wandhu wina. 10Bwanji, simdasome malembo yoyela?
‘Mwala udakanidwa ni mafundi omanga
chipano wakhala mwala wofunika kupitilila myala yonjhe yo mangila.
11Ambuye nde achita chindhu chimenecho,
Ni chindhu chimenecho chitidabwicha ife!’”
12Akulu wa ajhukulu, ni oyaluza thauko ni azee adajhiwa kuti chifani chimenecho chidali chanyiiwo. Amafuna kumgwila, nambho adaopa gulu la wandhu. Chimwecho adamsiyape ni kuchoka.
Nghani yo peleka malipilo
Matayo 22:15-22; Luka 20:20-26
13Pambuyo adaatuma Afalisayo akumojhi ni wandhu amamthangatila Helode, kuti akamfunjhe Yesu kwa kumchela icho siwakambe. 14Adampitila, ni kumkambila, “Oyaluza, tijhiwa kuti imwe mkamba uzene, ni simumuopa mundhu waliyonjhe, kapina ukulu wa mundhu, ni simupenya nghope ya mundhu. Nambho imwe muyaluza yayo wayafuna Mnungu wandhu ayachite. Tikambile bwanji, ni chindhu chabwino kapina osati chabwino kumpacha malipilo mfumu wa ku Loma kapina sitidampacha? Timlipe kapina tisidamlipa?” 15Nambho, Yesu wadaujhiwa ugunghuli wao, wadaafunjha, “Ndande yanji mnichela? Majhanayoni ndalama imeneyo niiyone.” 16Adampelekela ndalama imeneyo, ni iye wadafunjha, “Bwanji nghope ni jhina ili ni layani?” Ni anyiiwo adamuyangha, “Ni va mfumu wa ku Loma.” 17Ndipo, Yesu wadaakambila, “Va mfumu wa ku Loma mpacheni mfumu wa ku Loma, ni va Mnungu mpacheni Mnungu.” Adamzizwa Yesu kupunda.
Yesu wayaluza nghani yo hyuka
Matayo 22:23-33; Luka 20:27-40
18Ndiipo Masadukayo, wandhu yawo akamba kuti palibe kuhyuka, adampitila Yesu, ni adamfunjha, 19“Oyaluza, Musa wadatilamula chimwechi, ‘Mundhu wakamwalila ni kusiya wamkazi popande wana, mbale wake mundhu mmeneyo ifunika wamtenge wamkazi mmeneyo wafedwa ni mmunake, kuti wambalile wana mundhu mmeneyo.’ 20Kudali abale saba. Mkulu wao wadakwata ni kumwalila, popande kusiya mwana. 21Mbale wakawili wadamkwata yujha wamkazi wafedwa ni mmunake, nayenjho wadamwalila popande kusiya mwana. Chichijha mbale wakatatu wadamwalila popande kusiya mwana. 22Wonjhe saba adamwalila popande kusiya mwana. Pothela yujha wamkazi nayo wadamwalila. 23Chipano, wandhu yapo sahyuke, wamkazi mmeneyo siwakhale wamkazi wayani? Pakuti wonjhe saba adamkwata.”
24Yesu wadaayangha, “Anyiimwe mtaika ndande simjhiwa malembo yoyela kapina mbhavu za Mnungu. 25Wandhu akufa yapo siahyuke siakwata kapina kukwatiwa, siakhale ngati atumiki akumwamba a Mnungu. 26Nambho, nghani za kuhyuka, bwanji, simdasome chikalakala cha Musa nghani ya fukutu ilo limakwelela moto? Mnungu wadamkambila Musa, ‘Ine ni Mnungu wa Ibulahimu, Mnungu wa Isaka ni Mnungu wa Yakobo.’ 27Iye osati Mnungu wa wandhu akufa, nambho ni Mnungu wa wandhu amoyo. Chimwecho mtaikilatu.”
Lamulo lalikulu
Matayo 22:34-40; Luka 10:25-28
28Oyaluza mmojhi wa thauko wadafika, ni wadavela umo amachuchana. Yapo wadaona kuti Yesu wadaayangha bwino, wadamchata Yesu ni kumfujha, “Pamalamulo yonjhe, liti lamulo lalikulu kupitilila yonjhe?” 29Yesu wadamuyangha, “Lamulo lalikulu nde ili, ‘Velani imwe wandhu a ku Izilaeli! Ambuye Mnungu wathu, nde Ambuye mmojhipe. 30Akonde Ambuye Mnungu wako kwa mtima wako wonjhe, kwa mzimu wako wonjhe ni njelu zako zonjhe ni kwa mbhavu zako zonjhe.’ 31Ni lamulo lakawili nde ili ‘Mkonde mnjako ngati umo ujhikondela umwene.’ Palibe lamulo lina lili lalikulu kusiyana ni malamulo yaya yawili.”
32Yujha oyaluza thauko wadamkambila Yesu, “Oyaluza mwayangha bwino! Zenedi mwakamba bwino Mnungu ni mmojhi ni palibenjho Mnungu mwina. 33Umkonde Mnungu kwa mtima wonjhe, kwa njelu zonjhe ni kwa mbhavu zako zonjhe, ni kumkonda mnjako ngati umo ujhikondela umwene. Chindhu ichi chabwino kupitilila mahoka ni njhembe.”
34Yesu yapo wadaona kuti mundhu mmeneyo wamuyangha kwa njelu, wadamkambila, “Iwe uli pafupi kulowa muufumu wa Mnungu.”
Kuyambila pamenepo palibenjho mundhu uyo wadayesa kumfunjha funjho lina.
Kilisito ni yani
Matayo 22:41-46; Luka 20:41-44
35Yesu yapo wamayaluza panyumba ya Mnungu, wadaafunjha, “Ndande yanji oyaluza thauko akamba kuti Kilisito ni mwana wa mfumu Daudi? 36Mzimu Woyela udamchogoza Daudi nayo wadakamba,
‘Ambuye Mnungu adaakambila Ambuye wanga,
ukhale kujhanja langa la kwene,
mbaka waakhoze adani wako.’
37Daudi mwene wadamtana Kilisito ‘Ambuye,’ chipano Kilisito siwakhale bwanji mwana wa Daudi?”
Yesu wakaambila wandhu akhale maso ni oyaluza thauko
Matayo 23:1-36; Luka 20:45-47
Gulu lalikulu la wandhu limamvechela Yesu kwa chikondwelo 38Yesu yapo wamayaluza, wadakamba, “Khalani maso ni oyaluza thauko, anyiawo akonda kuvala njhalu zazitali ni kulonjeledwa ni wandhu mmalo yo komanilana wandhu ambili. 39Akonda kusangha mipando ya pachogolo panyumba zokomanilana Ayahudi ni kukhala malo ya ulemu mmaphwando. 40Anyiiwo alanda anyamaye yawo afedwa ni achamunao vyuma vawo, ajhichita anyiiwo abwino ni aphembhela popande kulema. Chimwecho sialamulidwe kopitilila.”
Maye wafedwa ni mmunake uyo wachocha njhembe bwino
Luka 21:1-4
41Yesu wadakhala pafupi ni chombo choikila njhembe panyumba ya Mnungu. Wadaona wandhu umo amachochela njhembe. Wopata ambili adachocha ndalama zambili. 42Pamenepo wadajha maye mmojhi wafedwa ni mmunake uyo wadali wosauka, wadachocha senti ziwili. 43Yesu wadaatana oyaluzidwa wake, ni kwaakambila, “Zenedi nikukambilani, maye uyu wosauka wachocha zambili kupitilila onjhe. 44Wandhu wonjhe achocha ivo vakhalila pachuma chao, nambho maye uyu wafedwa ni mmunake pamojhi ni kusauka kwake wachocha vonjhe walinavo.”
Àwon tá yàn lọ́wọ́lọ́wọ́ báyìí:
Maluko 12: NTNYBL2025
Ìsàmì-sí
Pín
Daako
Ṣé o fẹ́ fi àwọn ohun pàtàkì pamọ́ sórí gbogbo àwọn ẹ̀rọ rẹ? Wọlé pẹ̀lú àkántì tuntun tàbí wọlé pẹ̀lú àkántì tí tẹ́lẹ̀
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.