Yesu wadamuyangha, “Lamulo lalikulu nde ili, ‘Velani imwe wandhu a ku Izilaeli! Ambuye Mnungu wathu, nde Ambuye mmojhipe. Akonde Ambuye Mnungu wako kwa mtima wako wonjhe, kwa mzimu wako wonjhe ni njelu zako zonjhe ni kwa mbhavu zako zonjhe.’ Ni lamulo lakawili nde ili ‘Mkonde mnjako ngati umo ujhikondela umwene.’ Palibe lamulo lina lili lalikulu kusiyana ni malamulo yaya yawili.”