1
Marko 8:35
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
Marko 8:36
Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake?
3
Marko 8:34
Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata.
4
Marko 8:37-38
Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”
5
Marko 8:29
Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?” Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.”