1
Marko 9:23
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Yesu anati, “ ‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira.”
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
Marko 9:24
Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, “Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!”
3
Marko 9:28-29
Yesu atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali pa okha kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani ife sitinathe kutulutsa chiwandacho?” Iye anayankha kuti, “Mtundu uwu umatuluka pokhapokha mwapemphera ndi kusala kudya.”
4
Marko 9:50
“Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.”
5
Marko 9:37
“Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma.”
6
Marko 9:41
Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene akupatsani chikho cha madzi mʼdzina langa chifukwa ndinu ake a Khristu, sadzataya konse mphotho yake.”
7
Marko 9:42
“Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake.
8
Marko 9:47
Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena