Matayo 19
19
Nghani yosiyana
Maluko 10:1-12
1Yesu yapo wadamaliza kukamba nghani zimenezo, wadachoka kumujhi wa Galilaya ni kupita kumujhi wa Yudea, kuchijya la mchinje Yolodani. 2Gulu lalikulu la wandhu lidamchata, iye wadaalamicha.
3Afalisayo akumojhi adamchata Yesu ni kumfunjha kwa kumchela, “Bwanji, thauko limlola waamuna kumsiya mkazake ndande#19:3 ya cholakwa chilichonjhe?”
4Yesu wadaayangha, wadakamba, “Bwanji, simudasome Mmalembo Yoyela kuti poyamba Mnungu wadamuumba mundhu wammuna ni wamkazi? 5Mnungu wadakamba, ‘Pandande iyi mundhu wammuna siwaasiye atate wake ni maye wake ni kulunjana ni mkazake, ni awili yawa siakhale thupi limojhi.’ 6Chimwecho, anyiiwo osati awilinjho, nambho thupi limojhi. Icho wachilunjanicha Mnungu, mundhu siwadachisiyanicha.”
7Afalisayo adamfunjha, “Ndande yanji Musa wadaagiza wammuna wampache mkazake kalata yosiyana?”
8Yesu wadaayangha, “Musa wadakulolezani kwasiya achakazanu ndande anyiimwe ni wandhu yawo simuyaluzika, nambho siidali chimwecho yapo Mnungu wadaumba jhiko lapanjhi. 9Nikukambilani, mundhu waliyonjhe uyo siwamsiye mkazake popande ndande ya chigololo ni kukwata wamkazi mwina, mundhu mmeneyo wachita chigololo.”
10Oyaluzidwa wake adamkambila, “Ngati vindhu ivi vikakhala chimwechi pakati pa wammuna ni wamkazi, mbasa kukhala osakwate.”
11Yesu wadaakambila, “Osati wonjhe akhoza kuyalandila mau yaya, nambho anyiwajha Mnungu waapacha chindhu chimenecho. 12Kuli vindhu vambili ivo vaachita waachimuna asadakwata. Wina abadwa chimwecho, ni wina achitidwa chimwecho ni wandhu kuti siadakhala ni mbhavu zachimuna. Wina saakwata ndande ya Ufumu wa Mnungu. Mundhu uyo wakhoza kuyalandila mau yaya, wayalandile.”
Yesu waapacha mwayi wana wang'onoang'ono
Maluko 10:13-16; Luka 18:15-17
13Ndiipo wandhu wina adaapeleka wana waang'onoang'ono kwa Yesu kuti wasanjike manja ni kwaapembhela, nambho oyaluzidwa wake adaachekeleza wandhu wajha adaapeleka wana. 14Yesu wadaakambila, “Alekeni wana waang'onoang'ono ajhe kwaine, msachekeleza, pakuti Ufumu wa kumwamba ni wa wandhu ali ngati wanawa.”
15Ndiipo wadaasanjika manja ni kwaapembhela, ndiipo wadachokapo pa malo pamenepo.
Mnyamata wopata
Maluko 10:17-31; Luka 18:18-30
16Mundhu mmojhi wadamchata Yesu ni kumfunjha, “Oyaluza, nichite chiyani chabwino kuti nipate umoyo wa wosatha?”
17Yesu wadamfunjha, “Ndandeyanjii mnifunjha kuusu chindhu chabwino? Palibe mundu uyo wali wabwino nambho mmojhipe. Ukafuna kulowa mu umoyo wamuyaya, gwila thauko la Mnungu.”
18Mundhu yujha wadamfunjha, “Mathauko yati?”
Yesu wadamuyangha, “Usadapha, usadachita chigololo, usadaba, usadakamba mthila, 19alemekeze atate wako ni maye wako, ni mkonde mnjako ngati umo ujhikondela umwene.”
20Mnyamata yujha opata wadayangha, “Yaya yonjhe nayagwila, bwanji, nachepekela chiyani?”
21Yesu wadamuyangha, “Ngati ufuna ukhale ngati umo wafunila Mnungu, pita ukaguliche chuma chako chonjhe ni ndalamazo ukaagawile osauka, nawenjho siukhale ni chuma kumwamba, ndiipo unichate.”
22Mnyamatayo yapo wadavela chimwecho, wadabwelela kwao kwa chisoni, pakuti wadali ni chuma chambili.
23Pamenepo Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, “Zene nikukambilani, siikhale kolimba kwa mundhu wopata kulowa mu Ufumu wa kumwamba. 24Nikukambilaninjho, ikhozeka chinyama icho chitanidwa ngamila kupyola pa ndhoolo kasindano kusiyana ni mundhu wopata kulowa mu Ufumu wa Mnungu.”
25Oyaluza wake yapo adavela chimwecho adadabwa, adamfunjha, “Chipano ni yani uyo wakhoza kuomboledwa?”
26Yesu wadaapenyecha ni wadakambila, “Vindhu ivi kwa mundhu sivikhozekana, nambho kwa Mnungu vindhu vonjhe vikhozeka.”
27Ndiipo Petulo wadamuyangha, “Ife tasiya vonjhe ni kukuchata iwe. Bwanji, tipata chiyani?”
28Yesu wadaakambila, “Uzene nikukambilani, pa jhiko la mpya, Mwana wa Mundhu siwakhale pa mpando wa chifumu wa ulemelelo, anyiimwe mwanichata ine simukhale pamipando khumi ni iwili nimwaalamula mafuko khumi ni yawili ya Izilaeli. 29Mundhu walionjhe uyo wasiya nyumba yake, kapina achakulu wake kapina mlongo wake kapina atate wake kapina maye wake kapina wana kapina munda ndande ya ine, mmeneyo siwachuluchidwe kambili kwa vijha walinavo ni siwaupate umoyo wamuyaya. 30Nambho ambili yao ali oyamba saakhale othela ni wajha ali wothela saakhale oyamba.”
Actualmente seleccionado:
Matayo 19: NTNYBL2025
Destacar
Compartir
Copiar

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.