Matayo 16
16
Wandhu afuna vodabwicha
Maluko 8:11-13; Luka 12:54-56
1Afalisayo ni Asadukayo adamchata Yesu, adamuyesa kwa kumpembha waalangize vindhu vodabwicha kuchokela kumwamba. 2Nambho Yesu wadaayangha, “Ujhulo yapo ufika, mukamba, ‘Mawa kubwalo sikukhale bwino, ndande kumlengalenga kwafuwilila,’ 3Umawanjho mkamba, ‘Lelo mvula siinye ndande kumlengalenga kwafuwila ni mitambo yamanga.’ Anyiimwe mujhiwa umo kuliili kumlengalenga, nambho simukhoza kujhiwa vindhu ivo vichokela chipano kuti vili ni mate yanji. 4Wandhu ambadwa uno woipa ni wopande chikhulupi, ufuna vodabwicha! Nambho simpachidwa chodabwicha chilichonjhe kupitilila chijha chodabwicha cha Yona.”
Ndiipo Yesu wadaasiya ni kuchoka.
Amila ya Afalisayo ni Asadukayo
Maluko 8:14-21
5Oyaluzidwa wake yapo adayomboka kuchijya la nyanja, adazindikila kuti aiwala kutenga mabumunda. 6Yesu wadaakambila, “Khalani maso ni mjhipenyelele ni amila ya Afalisayo ni Asadukayo.”
7Ndiipo oyaluzidwa adayamba kukambilana achinawene kwa achinawene, “Wakamba chimwechi ndande sitidatenge mabumunda.”
8Yesu wadayajhiwa yayo amachuchana, wadaakambila, “Imwe, wandhu mukhulupilila pang'ono! Bwanji muchuchana mwachinawene ndande yosatenga mabumunda? 9Bwanji, mkalipe osajhiwe? Bwanji, simukumbukila mabunda yasano yajha nidapacha wandhu elufu zisano? Bwanji, mdajhaza miseche ingati ya vijha vokhalila? 10Kapina mabumunda saba yajha mudagaawila wandhu elufu zinayi, chiwelengelo cha miseche ingati mudakusa? 11Bwanji, simudajhiwa kuti sinimakambe nghani za mabumunda? Jhipenyeleleni ni amila ya Afalisayo ni Asadukayo.”
12Pamenepo oyaluzidwa wake adajhiwa kuti siwadakambile ajhipenyelele ndande ya amila ya mabumunda, nambho ajhipenyelele ni mayaluzo ya Afalisayo ni Asadukayo.
Petulo wakamba kuti Yesu nde Kilisito
Maluko 8:27-30; Luka 9:18-21
13Yesu yapo wadafika kumujhi wa Kaisaliya Filipi, wadaafunjha oyaluzidwa wake, “Bwanji, wandhu akamba kuti Mwana wa Mundhu ni yani?”
14Adamuyangha, “Wandhu wina akamba kuti ni Yohana Mbatizi, wina akamba kuti ni mlosi Elia ni wina akamaba kuti ni mlosi Yelemia kapina mmojhi wa alosi.”
15Yesu wadaafunjha, “Bwanji, ni anyiimwe mkamba kuti ine ni yani?”
16Simoni uyo watanidwa Petulo wadayangha, “Iwe nde Kilisito muomboli, Mwana wa Mnungu wali wamoyo.”
17Yesu wadayangha, “Wapachidwa mwawi iwe Simoni mwana wa Yona, pakuti ichi wachikamba siudavunukulilidwe ni mundhu, nambho Atate wanga a kumwamba. 18Niine nikukambila iwe Petulo, iwe ni mwala waukulu, ni pamwamba pa mwala umenewo, siniumange mpingo wanga, ni mbhavu za kumdima sizikhoza kulimbana nawo. 19Nikupacha ufunguo wa ufumu wa kumwamba ni chilichonjhe icho siuchimange pajhiko, sichimangidwe kumwamba, chilichonjhe icho siuchimasule pajhiko, sichimasulidwenjho kumwamba.”
20Ndiipo Yesu wadakaniza oyaluzidwa wake kuti siadamkambila mundhu waliyonjhe ngati iye wadali Kilisito.
Yesu wakamba kuusu kuvutika ni nyifa yake
Maluko 8:31; 9:1; Luka 9:22-27
21Kuyambila nyengo imeneyo Yesu wadayamba kuwakambila padanga oyaluzidwa wake, “Nifunika nipite kumujhi wa Yelusalemu, ni kumeneko sinivutichidwe kupunda kupitila mmanja ya waakulu ni akuluakulu wa ajhukulu, ni oyaluza a thauko, ni kumeneko siniphedwe, ni siku la katatu sinihyuke.”
22Pamenepo Petulo wadamtenga Yesu pambhepete, wadayamba kumnyindila, “Osati Ambuye, yaya siyadakupatani!” 23Yesu wadamng'anamukila Petulo ni kumkambila, “Choka pamaso panga, Satana! Iwe ni chochelekeza kwanga. Ndande maganizo yako siyachoka kwa Mnungu, nambho ni maganizo ya wandhu!”
24Ndiipo Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, “Mundhu uyo wafuna kunichata, poyamba wafunika wajhikane mwenewake ni kuutenga mtanda wake, wanichate. 25Pakuti, mundhu uyo wafuna kuulamicha umoyo wake, siwautaize, ni mundhu uyo siwautaize umoyo wake ndande ya ine, siwaupate. 26Pakuti, mundhu siwapate phindu lanji wakayapata yonjhe yali pajhiko, nambho wautaize umoyo wake? Kapina mundhu siwachoche chiyani kuti waupate umoyo wake? 27Pakuti, Mwana wa Mundhu siwajhe pa ulemelelo wa Atate wake pamojhi ni atumiki wake aku mwamba a Mnungu, ndeyapo siwamlipe kila mundhu kuchokana ni chijha wachichita. 28Zene nikukambilani, wandhu wina aima pano siamwalila mbaka yapo saamuone Mwana wa Mundhu niwajha mu Ufumu wake.”
Actualmente seleccionado:
Matayo 16: NTNYBL2025
Destacar
Compartir
Copiar

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.