Anyiimwe musadachita chimwecho, mmalo mwake, waliyonjhe uyo wafuna kukhala wamkulu pakati panu, wafunika wakhale mbowa wa wonjhe. Waliyonjhe uyo wafuna kukhala woyamba pakati panu wakhale mbowa wa wonjhe. Ngati umo ili kwa Mwana wa Mundhu siwadajhe kutumikilidwa, nambho kutumikila ni kuuchocha umoyo wake kwa kwaombola wandhu ambili.”