Yoweli 3:15-16

Yoweli 3:15-16 CCL

Dzuwa ndi mwezi zidzadetsedwa, ndipo nyenyezi sizidzawalanso. Yehova adzabangula kuchokera mu Ziyoni ndipo mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera mu Yerusalemu; dziko lapansi ndi thambo zidzagwedezeka. Koma Yehova adzakhala pothawira pa anthu ake, linga la anthu a ku Israeli.