Danieli 9:18-19
Danieli 9:18-19 CCL
Tcherani khutu, Inu Mulungu, ndipo imvani; tsekulani maso anu ndipo onani mabwinja athu ndi mzinda umene umadziwika ndi dzina lanu. Sitikupempha chifukwa chakuti ndife olungama, koma chifukwa cha kukula kwa chifundo chanu. Inu Ambuye imvani mawu athu! Ambuye khululukani! Ambuye timvereni, ndipo muchitepo kanthu! Kuti anthu adziwe kuti Inu ndinu Mulungu wanga musachedwe chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.”

