Danieli 8:19-21

Danieli 8:19-21 CCL

Iye anati, “Ine ndikuwuza zimene zidzachitike ukadzatha mkwiyo, chifukwa masomphenyawa ndi a nthawi ya chimaliziro.” Nkhosa yayimuna ya nyanga ziwiri imene unayiona, ikuyimira mafumu a Amedi ndi Aperezi. Mbuzi yayimuna ija ndi mfumu ya Agriki, ndipo nyanga yayikulu pakati pa maso ake aja ndi mfumu yoyamba.