1
Danieli 1:8
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Koma Danieli anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya ndi vinyo wa mfumu, ndipo anapempha chilolezo kwa mkulu wa nduna za mfumu kuti asadzidetse mwa njira imeneyi.
Compara
Explorar Danieli 1:8
2
Danieli 1:17
Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.
Explorar Danieli 1:17
3
Danieli 1:9
Ndipo Mulungu anafewetsa mtima wa ndunayo kuti amukomere mtima ndi kumuchitira chifundo Danieli
Explorar Danieli 1:9
4
Danieli 1:20
Nthawi zonse mfumu ikawafunsa zonse zofuna nzeru ndi chidziwitso, inkapeza kuti iwo anali oposa amatsenga ndi owombeza onse a mu ufumu wake wonse mopitirira muyeso.
Explorar Danieli 1:20