Maluko 16

16
Yesu wahyuka
Matayo 28:1-8; Luka 24:1-12; Yohana 20:1-10
1Yapo lidatha Siku lo Pumulila, Maliya wa ku Magidala ni Maliya maye wa Yakobo ni Salome, adagula mafuta yonunghila, adapita kulinyeka thupi la Yesu. 2Ndiipo umawamawa, siku la Jhumapili, adapita ku chiliza. 3Yapo adali mnjila adafunjhana, “Yani siwatigunghulichile mwala pakhomo la chiliza?” 4Yapo adawandikila kufika adapenya, adaona mwala ujha wasendezedwa patali ni khomo la chiliza. 5Chimwecho adalowa pachiliza, adamuona mnyamata uyo wadavala viwalo voyela, wakhala bendeka la kwene la chijha chiliza, anyiiwo adajhujhumuka kupunda.
6Mnyamata mmeneyo wadaakambila, “Simdajhujhumuka. Mumfunafuna Yesu wa ku Nazaleti uyo wadapachikidwa pamtanda. Wahyuka, balibepo pano. Penyani pamalo yapo adamgoneka. 7Chipano pitani mkaakambile oyaluzidwa popande kumyawalila Petulo, ‘Yesu wakuchogolelani ku Galilaya, kumeneko simumuone ngati umo wadakukambilani.’ ”
8Ndiipo adatuluka kubwalo kwa chiliza uku ni adatendhemela kwa mandha, adazizwa ni kuthamanga. Siadamkambile mundhu waliyonjhe chindhu chijha pakuti amaopa kupunda.
Yesu wamtulukila Maliya wa ku Magidala
Matayo 28:9-10; Yohana 20:11-18
9Yesu yapo wadahyuka umawamawa siku la Jhumapili, wadamtulukila uti Maliya wa kumujhi wa ku Magidala, uyo Yesu wadamchocha viwanda saba.#16:9 Bibiliya zina zilibe mzele wa tisa mbaka wa 20 10Maliya wa ku Magidala wadapita kwaakambila anyiwajha amalila ni kuimba zaya. 11Yapo adavela kuti Maliya wa ku Magidala wamwona Yesu wahyuka, siadakhulupilile.
Yesu watulukila oyaluzidwa awili
Matayo 28:16-20; Luka 24:36-49; Yohana 20:19-23
12Pambuyo Yesu wadaatulukila oyaluzidwa awili uku wali ni nghope ina. Oyaluzidwa achameneo amatopita kumunda. 13Yapo adamjhiwa, adabwela ni kupita kwaakambila achanjao, nambho anyiiwo siadakhulupilile.
Yesu watulukila oyaluzidwa wake khumi ni mmojhi
Matayo 28:16-20; Luka 24:36-49; Yohana 20:19-23
14Pambuyo Yesu wadatulukila oyaluzidwa khumi ni mmojhi yapo amadya chakudya. Yesu wadaanyindila ndande ya kulimba kwa mitima yao, ni ndande yakusiya kwaakhulupilila anyiwajha adamuona yapo wadahyuka. 15Chimwecho wadaakambila, “Pitani kujhiko lonjhe la panjhi, mkalalikile wandhu wonjhe Uthenga Wabwino. 16Mundhu waliyonjhe uyo wakhulupilila ni kubatizidwa, siwaomboledwe, nambho mundhu uyo wakana kukhulupilila siwalamulidwe. 17Vizindikilo ivi sivikhale pamojhi ni anyiiwo siakhulupilile. Satumile mbhavu za jhina langa kuchocha viwanda ni kukamba kwa mkambo wina. 18Akagwila njoka kapina kumwa chalichonjhe chili ni sumu sichawenga. Siwaikile manja wandhu wodwala, nawo saalame.”
Yesu watengedwa kupita kumwamba
Luka 24:50-53
19Ambuye Yesu yapo adamaliza kukamba ni oyaluzidwa wawo, adatengedwa kupita kumwamba, adakhala kubendeka la kwene la Mnungu. 20Ndiipo oyaluzidwa wajha adapita kummalo yonjhe kwa lalikila wandhu Uthenga wa Bwino. Ambuye Yesu adachita njhito pamojhi ni anyiiwo ni kuchimikiza uthenga umenewo kwa vizindikilo ivo vidalingana Uthenga umenewo.

Àwon tá yàn lọ́wọ́lọ́wọ́ báyìí:

Maluko 16: NTNYBL2025

Ìsàmì-sí

Pín

Daako

None

Ṣé o fẹ́ fi àwọn ohun pàtàkì pamọ́ sórí gbogbo àwọn ẹ̀rọ rẹ? Wọlé pẹ̀lú àkántì tuntun tàbí wọlé pẹ̀lú àkántì tí tẹ́lẹ̀