1
Luka 2:11
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
Luka 2:10
Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse.
3
Luka 2:14
“Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba, ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo.”
4
Luka 2:52
Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.
5
Luka 2:12
Ichi chidzakhala chizindikiro kwa inu: mukapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera ngʼombe.”
6
Luka 2:8-9
Ndipo kunali abusa amene amakhala ku dera lomwelo, kuyangʼanira ziweto zawo usiku. Mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iwo ndipo ulemerero wa Ambuye unawala mowazungulira. Iwo anachita mantha.