Eksodo 8:18-19
Eksodo 8:18-19 CCL
Koma amatsenga atayesa kupanga nsabwe mwa matsenga awo, analephera. Ndipo nsabwezo zinali pa munthu aliyense ndi pa ziweto zawo. Amatsenga anati kwa Farao, “Izi wachita ndi Mulungu.” Koma mtima wa Farao unali wowumabe ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananenera.


