Eksodo 7:11-12
Eksodo 7:11-12 CCL
Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Aliyense wa iwo anaponya ndodo yake pansi ndipo inasanduka njoka. Koma ndodo ya Aaroni inameza ndodo zawo.

