Eksodo 32:7-8
Eksodo 32:7-8 CCL
Pamenepo Yehova anati kwa Mose, “Tsika msanga, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto aja adziyipitsa kwambiri. Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, ‘Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”


