1
MARKO 2:17
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
Ndipo pamene Yesu anamva ichi, ananena nao, Akulimba safuna sing'anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.
ႏွိုင္းယွဥ္
MARKO 2:17ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
2
MARKO 2:5
Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa.
MARKO 2:5ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
3
MARKO 2:27
Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata
MARKO 2:27ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
4
MARKO 2:4
Ndipo pamene sanakhoze kufika kuli Iye, chifukwa cha khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo.
MARKO 2:4ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
5
MARKO 2:10-11
Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira machimo pa dziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje), Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu.
MARKO 2:10-11ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
6
MARKO 2:9
Chapafupi nchiti, kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?
MARKO 2:9ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
7
MARKO 2:12
Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.
MARKO 2:12ရွာေဖြေလ့လာလိုက္ပါ။
ပင္မစာမ်က္ႏွာ
သမၼာက်မ္းစာ
အစီအစဥ္မ်ား
ဗီဒီယိုမ်ား