Logo de YouVersion
Icono de búsqueda

Matayo Mau ya uchogolelo

Mau ya uchogolelo
Uthenga wabwino umo walembedwa ni Matayo ni chimojhi pa vikalakala vinayi mu chipangano chachipano vilangiza ukhalo wa Yesu Kilisito. Kila chimojhi chitanidwa Injili Mateyake Uthenga wabwino. Vikalakala ivi vidalembedwa ni Matayo ni Luka ni Maluko ni Yohana pambuyo pa nyifa ya Yesu. Osoma saajhiwa liti Injili ya Matayo idalembedwa. Nambho akhaikila kuti idalembedwa vyaka vya sitini pambuyo pa kubadwa kwa Yesu. Malo yayo idalembedwela Injili siyajhiwika. Nambho wandhu ambili akhaikila kuti idalembedwa ku jhiko la Palesitina ni ikhozeka mmujhi wa Yelusalemu.
Chikalakala ichi chidalembedwa ni Matayo uyo wamalandila malipilo nyengo Yesu wakali osamtana kukhala oyaluzidwa wake. Chinchijha Matayo wamajhiwikanjho kwa jhina la Lawi. Matayo ni mmojhi pakati pa atumwi khumi ni awili ni wadaalembela osoma Achiyahudi. Nghani iyi ichimikizidwa kupitilila nukuu sitini ya malembo ina ya chipangano cha kale. Matayo wamafuna kukamba kuti Yesu wadali Mesiya. Muomboli uyo wasanghidwa ni Mnungu uyo ulosi udafotokoza nghani zake. Matayo walembanjho vina kuusu Ufumu wa Mnungu. Ayahudi adayembekeza kuti Mesiya siwakhale Mfumu wa jhiko. Chimchijha Matayo wadalemba yambili kuchuchana ni maganizo yao pa kwaafotokozela Ufumu wa Chizimu wa Mnungu.
Uthenga Wabwino umo udalembedwa ni Matayo ni chikalakala chabwino kukhala mmayambo mwa chipangano chachipano ndande chibwelelanjho nghani izo zili muchipangano cha kale. Chilunjanicho chabwino icho chalunjanicha vipangano viwili. Osoma nao afotokoza kuti Matayo wamayesa kuchatiza malembedwe ya vikalakala va Musa ivo vili visano voyambila muchipangano cha kale. Yesu wali ku phili 5-7 ikhoza kulinganichidwa ni Mnungu wamampacha Musa lamulo. Chikumbukilo 19:3-23, 33.
Yayo yalimo mchikalakala ichi
Matayo wauyamba Uthenga wabwino kwa kufotokoza kuusu kubadwa kwa Yesu Kilisito ni kuyamba kwa njhito yake. Musula ya 1-4.
Ndiipo Matayo wafotokoza njhito ya Yesu ni mayaluzo yake. Musula ya 5-25.
Malo yothela ya Uthenga wabwino umo wadalembela Matayo yalangiza chindhu chachikulu kupunda cha kumwalila ni kuhyuka kwa Yesu. Musula ya 26-28.

Actualmente seleccionado:

Matayo Mau ya uchogolelo: NTNYBL2025

Destacar

Compartir

Copiar

None

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión