Logo de YouVersion
Icono de búsqueda

Matayo 20

20
Ochita njhito mmunda wa mizabibu
1“Ufumu wa kumwamba ulingana ni mwene munda uyo wadachoka umawawa, wadapita kwaafunafuna wandhu akachite njhito mmunda wake wa mizabibu. 2Wadavomela kwaalipa ndalama ya njhito ya siku limojhi, ndiipo wadaapeleka mmunda mwake akachite njhito. 3Pambuyo pa masaa yatatu umawa, wadaapheza wandhu wina aima pamalo yokomanilana wandhu ni alibe njhito. 4Wadaamkambila, ‘Anyiimwe namwenjho mapitani mukachite njhito kumunda wanga wa zabibu, nane sinikulipeni mkokolo wanu ngati umo ifunikila.’ 5Ndiipo adapita pamojhi. Mwene munda yujha wadachokanjho saa sita ni saa tisa, wadachita chinchijha ngati umo wadachitila poyamba. 6Yapo idakwana saa khumi namojha ujhulo, wadachokanjho ni kukomana ni wandhu wina aima pamalo yogulichila malonda. Basi, wadaafunjha, ‘Ndandeyanji mwaima pano usana wonjhewu popande njhito?’ 7Anyiiwo adamuyangha, ‘Palibe uyo watupacha njhito,’ Nayo wadaakambila, ‘Anyiimwe namwenjho pitani mkachite njhito ku munda wanga wa zabibu.’
8“Ujhulo yapo udafika, mwene munda yujha wadamkambila woimilila wake, ‘Atane ochita njhito waalipe ndalama zao, uyambe ni othela ndiipo achate wajha adachogolela kuchita njhito.’ 9Wandhu adachita njhito kuyambila saa khumi na mojha, kila mmojhi wadalipidwa mkokolo wake wa siku limojhi. 10Anyiwajha adachogolela kuchita njhito yapo adajha, amaganiza kuti saapachidwe papakulu, nambho naonjho adalandila kila mmojhi mkokolo umweujha wa siku limojhi. 11Yapo adalandila mkokolo wao, adayamba kumdandaulila yujha mwene munda. 12Adakamba, ‘Anyiyawa achita njhito mmathelo, achita njhito kwa saa imojhipe, ndandeyanji alandila mkokolo wolingana ni ife, tachita njhito siku lambhumbhu pajhuwa?’ 13Pamenepo yujha mwene munda wadamuyangha mmojhi wao, ‘Bwenji langa, sinidakuchefye. Bwanji, sitidavomelezane kukupachani mkokolo wa siku limojhi? 14Tenga chili chako ujhipita. Nifuna kumpacha uyu wothela ngati umo nakupachila iwe. 15Bwanji, osati bwino ine kuchita icho nifuna kuchita kwa ndalama zanga? Bwanji, kapina uwona njhanje ndande ine nili ni mtima wabwino?’”
16Yesu wadamalizila pokamba, “Chimwecho wothela siwakhale oyamba ni woyamba siwakhale wothela.”
Yesu wakamba ka katatu nghani za kufa kwake
Maluko 10:32-34; Luka 18:31-34
17Yesu yapo wamapita kumujhi wa Yelusalemu, wadaatenga oyaluzidwa wake khumi ni awili kumalo kopande wandhu, wadakambila, 18“Velani! Tupita ku yelusalemu, kumeneko Mwana wa Mundhu siwapelekedwe kwa wakulu ajhukulu ni oyaluza thauko, anyiiwo siamlamule kuphedwa. 19Ndiipo saampeleke kwa wandhu yawo osati Ayahudi siamchite chipongwe ni kumkwapula mikwapulo ni siamphe kwa kumpachika pamtanda, ni siku lakatatu siwahyuke.”
Maye wa Yakobo ni Yohana wampembha Yesu chindhu
Maluko 10:35-45
20Ndiipo, maye wa wana a Zebedayo pamojhi ni wana wake adajha kwa Yesu, wadagwada pachogolo pake ni kumpembha wamchitile icho wachifuna.
21Yesu wadamfunjha, “Ufuna chiyani?”
Wamkazi yujha wadakamba, “Chonde nikambile uzene, wana wanga awiliwa akhale mmojhi ku jhanja la manjele ni mwina ku jhanja la kwene ku Ufumu wako.”
22Yesu wadaakambila, “Simujhiwa icho mupembha, bwanji, mukhoza kumwela chikho cha mavuto ngati icho sinimwele ine?”
Anyiiwo adamuyangha, “Tikhoza,”
23Yesu wadaakambila, “Zene simchimwele chikho cha mavuto ngati umo sinichimwele ine, nambho nilibe lamulo yosangha yani wakhale ku manjele kwanga kapina kwene kwanga. Malo yameneyo yaikidwa ndande ya anyiwajha asanghidwa ni Atate wanga.”
24Oyaluzidwa wina khumi awili yapo adavela chimwecho wadaakwiyila kupunda Yakobo ni Yohana. 25Nambho Yesu wadaatana wonjhe pamojhi, wadakambila, “Mujhiwa kuti alamuli awandhu yawo osati Ayahudi, alamula wandhu wao kwa mbhavu ni wandhu wao ali ni ulamulilo kwao. 26Anyiimwe musadachita chimwecho, mmalo mwake, waliyonjhe uyo wafuna kukhala wamkulu pakati panu, wafunika wakhale mbowa wa wonjhe. 27Waliyonjhe uyo wafuna kukhala woyamba pakati panu wakhale mbowa wa wonjhe. 28Ngati umo ili kwa Mwana wa Mundhu siwadajhe kutumikilidwa, nambho kutumikila ni kuuchocha umoyo wake kwa kwaombola wandhu ambili.”
Yesu waalamicha osapenya awili
Maluko 10:46-52; Luka 18:35-43
29Yesu ni oyaluzidwa wake yapo amachoka kumujhi wa Yeliko, gulu lalikulu la wandhu lidamchata. 30Osapenya awili adakhala mmbhepete mwa njila. Yapo adavela kuti Yesu wapita pamenepo, adabula phokoso niakamba, “Ambuye, Mwana wa Daudi, tilengele lisungu!”
31Gulu lijha lidaanyindila ni kwaakambila akhale chete. Nambho anyiiwo adayendekela kutanilila niakamba, “Ambuye, Mwana wa Daudi, tilengele lisungu!”
32Yesu wadaima ni kwaatana, wadaafunjha, “Mfuna nikuchitileni chiyani?”
33Adamuyangha, “Ambuye, tifuna kupenya!”
34Yesu wadaalengela lisungu ni wadaagafya maso yao. Pampajha adakhoza kupenya, nawo adamchata.

Actualmente seleccionado:

Matayo 20: NTNYBL2025

Destacar

Compartir

Copiar

None

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión