Matayo 17
17
Yesu wang'anamuka nghope
Maluko 9:2-13; Luka 9:28-36
1Yapo yadapita masiku sita, Yesu wadaatenga Petulo, Yakobo ni Yohana mbale wa Yakobo, wadaatenga anyiiwo okha nikupitanao pa pamalo ya chisisi. 2Kumeneko, Yesu wadang'anamuka nghope pamaso pawo, nghope yake idali yophulikila ngati jhuwa ni njhalu zake zidali zoyela mbee. 3Ndiipo, Musa ni Eliya adaatulukila pachogolo pao, adakamba ni Yesu. 4Ndiipo Petulo wadamkambila Yesu, “Ambuye, siikhale bwino ngati sitikhale pano! Ngati mukonda sinimange visakasa vitatu, chimojhi chanu, chimojhi cha Musa ni chimojhi cha Eliya.”
5Petulo yapo wamakamba chimwecho, mtambo wong'azikila udavinikila, ni mvekelo udaveka kuchoka kumtambo, “Uyu nde Mwana wanga uyo nimkonda, nikondwela nayo kupunda, mveleni iye.”
6Oyaluzidwa wake yapo adavela mvekelo ujha adagwa chifufumimba, adaopa kupunda. 7Yesu wadaachata ni kwaagafya, wadaakambila, “Ukani, msadaopa!” 8Yapo adapenya, sadamwuone mundhu mwina waliyonjhe, nambho Yesu yokhape.
9Yapo amachika phili, Yesu wadanyindila, “Msadaakambila wandhu wina yaya mwayaona mbaka yapo Mwana wa Mundhu siwahyuke.”
10Oyaluzidwa wake adaamfunjha, “Ndande yanji oyaluza a thauko akamba kuti Eliya ifunika wajhe uti?”
11Yesu wadaayangha, “Zenedi, Eliya siwajhe uti, nayo siwavichite vindhu vonjhe kuti vikhale tayali. 12Nambho nikukambilani, Eliya wathokujha ni anyiiwo siadamjhiwe, ni anyiiwo adamchita umo adafunila. Chinchijha, Mwana wa Mundhu siwavutichidwe mmanja mwao.”
13Ndiipo oyaluzidwa adajhiwa kuti wamaakambila nghani za Yohana Mbatizi.
Yesu wamlamicha mnyamata wachiwanda
Maluko 9:14-29; Luka 9:37-43
14Yapo adafika pa gulu la wandhu, mundhuu mmojhi wadamchata Yesu, wadamgwadila, 15wadamkambila, “Ambuye mnilengele lisungu, mwanawanga wali ni njilinjili, ni wavutika kupunda. Ndhawi zambili wagwela pamoto kapina mmajhi. 16Nidampeleka kwa oyaluzidwa wako nambho siadakhoze kumlamicha.”
17Yesu wadaayangha, “Imwe mbadwa wopande chikhulupi ni olakwa! Sinikhale ni anyiimwe mbaka liti? Sinikulimbileni mtima mbaka liti? Jhinayoni pano mnyamatayo.” 18Ndiipo Yesu wadachinyindila chiwanda, nacho chidamchoka mnyamata, ni wadalama pampajha.
19Ndiipo oyaluzidwa adamchata Yesu kwa yokha, adaamfunjha, “Ndande yanji ife tidalepela kutopola chiwanda chijha?”
20Yesu wadaayangha, “Ndande ya chikhulupi chanu chochepa. Nikukambilani uzene, ngati mdakakhala ni chikulupi ngati mbeu ya aladali, mdakakhoza kulikambila phili ili, ‘Chokapo upite yapo’ nalo udakapita. Palibe chindhu icho sichilepeleke kwanu. 21Chiwanda cha mtundu uwu sichikhoza kuchochedwa kwa njila iliyonjhe, nambho kwa kumanga ni kupemdhela.”
Yesu wakambanjho nghani za nyifa yake ni kuhyuka kwake
Maluko 9:30-32; Luka 9:43-45
22Siku limojhi yapo adali pamojhi kujha ku Galilaya, Yesu wadaakambila, “Mwana wa Mundhu siwagwilidwe ni kupelekedwa kwa wandhu. 23Anyiiwo saamphe, nambho siku la katatu siwahyuke.”
Ni oyaluzidwa wake sadandaule kupunda.
Kuchocha nsongho mnyumba ya Mnungu
24Yesu ni oyaluzidwa wake yapo adafika ku Kapelinaumu, wandhu alandila nsongho wa mnyumba ya Mnungu adamchata Petulo ni kumfunjha, “Bwanji, oyaluza wanu wachocha nsongho wa mnyumba ya Mnungu?”
25Petulo wadayangha, “Yetu, wachocha.”
Petulo yapo wadalowa mkati, Yesu wadayamba kumfunjha, “Simoni, iwe uona bwanji? Mafumu ajhiko alandila malipilo ni nsongho kuchoka kwa ayani? Kwa wandhu wao kapina kuchokela kwa alendo?”
26Petulo wadamuyangha Yesu, “Kuchoka kwa alendo.”
Yesu wadamkambila, “Ni bwino, wandhu wao saafunika kuchocha nsongho. 27Nambho sitifuna kwaakwiicha wandhu anyiyawa, pita kunyanja ukawejhe, utenge njhomba yoyamba kukodwa, uiyasamiche kamwa lake, ni mkati mwake siukomane ndalama. Itenge ukalipile nsongho yaine ni ukajhilipile iwe.”
Actualmente seleccionado:
Matayo 17: NTNYBL2025
Destacar
Compartir
Copiar

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: