Logo de YouVersion
Icono de búsqueda

Matayo 15

15
Mayaluzo kuchokela kwa azee
Maluko 7:1-13
1Ndiipo Afalisayo akumojhi ni oyaluza athauko kuchokela ku Yelusalemu, adamchata Yesu ni kumfunjha, 2“Ndande yanji oyaluzidwa wako saachata mayaluzo yayo taulandila kuchokela kwa azee wathu? Pakuti saasamba bwino manja yao mbaka mvigwinghwi ngati umo ifunikila akali osadye!”
3Yesu wadaayangha, “Ndande yanji namwenjho simuchata thauko la Mnungu nambho mchata mayaluzo yanu? 4Mnungu wakamba, ‘Waalemekeze atate wako ni maye wako’ ni ‘Waliyonjhe uyo waatukwana atate wake kapina maye wake, waphedwe.’ 5Nambho anyiimwe muyaluza kuti ngati mundhu wali ni chindhu chalichonjhe icho wakhoza kwathangatila atate wake kapina amaye, nambho wakamba, ‘Chindhu ichi namchochela Mnungu,’ 6anyiimwe muyaluza mundhu mmeneyo siwafunika kwaalemekeza atate wake ni amake. Chimwecho nde umo mulidelela mawu la Mnungu kwa kuchata mayaluzo yanu mwachinawene wake. 7Agunghuli anyiimwe! Mlosi Isaya wadalosela bwino nghani zanu, yapo wadakamba kuusu anyiimwe,
8‘Mnungu wakamba kuti wandhu anyiyawa anilemekeza kwa maupe,
nambho mmitima mwao alipatali ni ine.
9Kunilambila kwao kulibe mate,
pakuti ayaluza mayaluzo ya wandhu ngati mayaluzo yanga!’”
Vindhu ivo vimchita mundhu siwadavomelezeka pa kumlambila Mnungu
Maluko 7:14-23
10Ndiipo Yesu wadalitana gulu la wandu lijha, wadalikambila, “Mnivechele ni mvanenavo! 11Osati chijha chimlowa mkamwa nde icho chimchita mundhu siwadavomelezeka kwa kumlambila Mnungu, nambho chijha chimchoka mundhu nde icho chimchita siwadavomelezeka pakumlambila Mnungu.”
12Ndiipo oyaluzidwa adamjhela ni kumfunjha, “Bwanji, ujhiwa Afalisayo pajha avela nghani ijha adakwiya?”
13Yesu wadaayangha, “Mmela uliwonjhe uwo siadauvyale Atate wanga akumwamba siuzulidwe. 14Msadavechela, achameneo ni achogoleli wa osapenya, ni osapenya wakamchogoza osapenya mnjake, wonjhe awili saabile mjhenje.”
15Petulo wadamkambila, “Tikambileni mate ya chifani chimenecho.”
16Yesu wadaafunjha, “Bwanji, anyiimwe namwenjho simjhiwa nghani imeneyi? 17Bwanji, simujhiwa kuti chilichonjhe icho chilowa mkamwa chipitilila mmimba ni mathelo yake chipita kudambo? 18Nambho chindhu icho chituluka mkamwa chichoka mumtima, chimenecho nde icho chimchita mundhu siwadavomelezeka pakumlambila Mnungu. 19Pakuti mumtima yachoka maganizo ya kupha, chigololo, uhule, unami, kuba, umboni wanthila ni matukwano. 20Yaya nde yayo yamchita mundhu siwadavomelezeka pa kumlambila Mnungu. Nambho kudya chakudya kwa manja yayo siyadasambidwe bwino mbaka mvigwinghwi siyamchita mundhu siwadavomelezeka pa kumlambila Mnungu.”
Chikhulupi cha wamkazi
Maluko 7:24-30
21Yesu wadachoka malo yameneyo ni kupita kumijhi ya Tilo ni Sidoni. 22Wamkazi mmojhi uyo wamakhala mmalo yameneyo, uyo siwadali Myahudi, wadamchata Yesu uku niwalila, niwakamba, “Nilengele lisungu iwe Mwana wa Daudi, mwali wanga wazamwa ni viwanda, wavutika kupunda.”
23Nambho Yesu siwadamuyanghe mau lililonjhe. Chimwecho oyaluzidwa wake adamchata ni kumpembha kupunda, “Mkambile wachoke ndandeyake watichata uku niwatibulila phokoso.”
24Yesu wadaayangha, “Ine natumidwa kwa wandhu ajhiko la Izilaeli yawo ali ngati mbelelepe izo zataika.”
25Wamkazi yujha wadajha ni kumgwadila Yesu, niwapembha, “Pepani Ambuye mnithangatile.”
26Yesu wadayangha, “Osati bwino kutenga chakudya cha wana ni kwaaponyela agalu.”
27Wamkazi yujha wadayangha, “Yetu Ambuye, nambho ata agalu akudya vakudya ivo vikugwa panjhi mbuye wake yapo wakudya.”
28Ndiipo Yesu wadamuyangha, “Wamkazi iwe, chikhulupi chako chachikulu, siuchitilidwe icho udachipembha.” Pampajha mwali wake wadalama.
Yesu waalamicha wandhu ambili
29Yesu wadachokapo pa malo yajha ni kupita mbhepete mwa nyanja ya Galilaya. Wadakwela kuphili ni kukhala panjhi. 30Gulu lalikulu la wandhu lidamchata, ni adampeleka wandhu osayende, osapenya, wosakhoze kukamba ni wina ambili adamuikila pachogolo pake, ni wonjhe wadaalamicha. 31Gulu la wandhu wajha lidadabwa yapo adaona wandhu osakhoze kukamba niakamba, osayenda niayenda, wovuwala nialama, nawo adamtamanda Mnungu wa Izilaeli.
Yesu waapacha chakudya wandu alufu zinai
Maluko 8:1-10
32Ndiipo Yesu wadaatana oyaluzidwa wake ni kwaakambila, “Nililengela lisungu gulu ili la wandhu, ndande yake akhala ni ine kwa masiku yatatu, ni chipano alibe chakudya icho chakhalila. Ine sinifuna kwaalaila akali ni njala, akhoza kukomoka mnjila.”
33Oyaluzidwa wake adaafunjha, “Pano tili ni paphululu, bwanji, sitipate kuti chakudya chokhoza kwaakwanila wandhu wonjhewa?”
34Yesu wadaafunjha, “Muli ni mabumunda yangati?”
Anyiiwo adayangha, “Mabunda saba ni njhomba zazing'onozing'ono zochepa.”
35Yesu wadalikambila gulu la wandhu lijha likhale panjhi. 36Ndiipo wadatenga mabumunda yajha saba ni njhomba zijha, wadamuyamika Mnungu, wadabandula ni kwaapacha oyaluzidwa wake, nawo wadaagawila wajha wandhu. 37Wandhu wonjhe adadya ni kukhuta. Ndiipo oyaluzidwa wake adakusa vijha vidakhalila nikujhaza miseche saba. 38Waachimuna yawo adadya adali ngati elufu zinayi, waachikazi ni wana siadawelengedwe.
39Ndiipo Yesu wadaalaila wandhu, iye wadakwela bwato waukulu ni kupita kumujhi wa Magadani.

Actualmente seleccionado:

Matayo 15: NTNYBL2025

Destacar

Compartir

Copiar

None

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión