Yesu wadabadwa ku mujhi wa Beselehemu mjhiko la Yudea. Ndhawi imeneyo Helode wadali mfumu. Yesu yapo wadandobadwa wandhu yawo amajhiwa icho sichichokele adafika ku Yelusalemu adaafunjha, “Walikuti mwana uyo wabadwa Mfumu wa Ayahudi? Pakuti tayiona ndhondwa yake kudela la kumwela ni nafenjho tajha kumulambila.”