YouVersion Logo
Search Icon

Mt. 1

1
Makolo a Yesu Khristu
(Lk. 3.23-38)
1Yesu#1.1 Yesu: Dzina limeneli limatanthauza kuti, “Ambuye ndi chipulumutso.” Khristu,#1.1 Khristu: Mau ameneŵa achigriki amatanthauza kuti, “Wodzozedwa.” Onani Matanthauzo a Mau. makolo ake anali Davide ndi Abrahamu. Motsatanatsatana maina a makolo ake onse ndi aŵa:
2Abrahamu adabereka Isaki, Isaki adabereka Yakobe, Yakobe adabereka Yuda ndi abale ake. 3Yuda adabereka Perezi ndi Zera, mwa Tamara; Perezi adabereka Hezironi, Hezironi adabereka Ramu. 4Ramu adabereka Aminadabu, Aminadabu adabereka Nasoni, Nasoni adabereka Salimoni. 5Salimoni adabereka Bowazi mwa Rahabu, Bowazi adabereka Obede mwa Rute, Obede adabereka Yese, 6#2Maf. 24.14, 15; 2Mbi. 36.10; Yer. 27.20Yese adabereka mfumu Davide.
Davide adabereka Solomoni, mwa amene poyamba adaali mkazi wa Uriya. 7Solomoni adabereka Rehobowamu, Rehobowamu adabereka Abiya, Abiya adabereka Asa. 8Asa adabereka Yehosafati, Yehosafati adabereka Yoramu, Yoramu adabereka Uziya. 9Uziya adabereka Yotamu, Yotamu adabereka Ahazi, Ahazi adabereka Hezekiya. 10Hezekiya adabereka Manase, Manase adabereka Amoni, Amoni adabereka Yosiya. 11Yosiya adabereka Yekoniya ndi abale ake, pa nthaŵi imene Aisraele adaatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni.
12Aisraele atatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, Yekoniya adabereka Salatiele, Salatiele adabereka Zerubabele. 13Zerubabele adabereka Abihudi, Abihudi adabereka Eliyakimu, Eliyakimu adabereka Azoro. 14Azoro adabereka Zadoki, Zadoki adabereka Akimu, Akimu adabereka Eliudi. 15Eliudi adabereka Eleazara, Eleazara adabereka Matani, Matani adabereka Yakobe. 16Yakobe adabereka Yosefe, mwamuna wa Maria. Mariayu adabala Yesu, wotchedwa Khristu.
17Choncho panali mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Abrahamu mpaka pa mfumu Davide, mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Davideyo mpaka pa nthaŵi imene Aisraele adaatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, ndiponso mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa nthaŵi yotengedwa ukapolo kupita ku Babiloni mpaka pa nthaŵi ya Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
Kubadwa kwa Yesu Khristu
(Lk. 2.1-7)
18 # Lk. 1.27 Kubadwa kwa Yesu Khristu kudaatere: amai ake Maria adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe; koma asanaloŵane, Maria adaapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mphamvu za Mzimu Woyera. 19Mwamuna wake Yosefe anali munthu wokonda chilungamo, komabe sadafune kumchititsa manyazi poyera. Nchifukwa chake adaganiza za kungothetsa mbeta ija osachitapo mlandu. 20Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuwonekera m'maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. 21#Mphu. 46.1; Lk. 1.31Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.”
22Zonsezi zidaatero kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, 23#Yes. 7.14“Namwali wina wosadziŵa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.”
24Tsono Yosefe atadzuka, adachita monga momwe mngelo wa Ambuye uja adaamuuzira. Adamtenga Maria, mkazi wake uja, 25#Lk. 2.21koma sadamdziŵe mpaka adabala mwana wamwamuna. Pambuyo pake Yosefe adatcha mwanayo dzina loti Yesu.

Currently Selected:

Mt. 1: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy