Maluko 14

14
Njila yakumpha Yesu
Matayo 26:1-5; Luka 22:1-2; Yohana 11:45-53
1Zidakhalila siku ziwili kulowa siku la pwando la Pasaka ni ya mabumunda yayo siidathilidwe amila. Wakuluakulu a ajhukulu, ni oyaluza athauko amamafuna funa njila ya kumgwila Yesu kwa chisisi ni kumpha. 2Adakamba, “Sitidamgwila ndhawi ya pwando la Pasaka, pakuti wandhu akhoza kuchita fujho.”
Wamkazi wamnyeka Yesu mafuta ku Besania
Matayo 26:6-13; Yohana 12:1-8
3Yesu wadali ku Besania kukhomo kwa Simoni, uyo wadali ni makate. Yapo amadya chakudya cha ujhulo, wamkazi mmohji, uyo wadali ni njhupa iyo idali ni mafuta yonunghila ya mtengo wa ukulu, wadajha, wadamasula ijha njhupa ni kumpungulila Yesu kumutu. 4Wandhu akumohji adali pamenepo adakwiya, adakambilana, “Ndande yanji wawananga mafuta ya mtengo waukulu kupunda? 5Mbasa yadakagulichidwa kwa mtengo waukulu kupunda, ni ndalama zimenezo kwapacha osauka.” Ndiipo adamnyindila yujha wamkazi.
6Nambho Yesu wadaakambila, “Msiyeni! Ndande yanji mumchaucha? Iye wanichitila chindhu cha bwino. 7Wandhu osauka mulinao siku zonjhe, mkhoza kwathangatila ndhawi yaliyonjhe yapo mfuna. Nambho ine sinikhala ni anyiimwe siku zonjhe. 8Wamkazi uyu wachita umo wakhozela, ni wachogolela kulinyeka thupi langa mafuta ndande yo kulikonjekela likali losazikidwe 9Nikukambilani uzene, paliponjhe pajhiko Uthenga Wabwino yapo siilalikidwe, chindhu ichi wachichita uyu maye sichichuludwe kwa kumkumbukila Iye.”
Yuda wavomela kumng'anamuka Yesu
Matayo 26:14-16; Luka 22:3-6
10Ndiipo, Yuda isikaliyote, mmojhi wawajha oyaluzidwa khumi ni awili, wadapita kwa wakulu wa jhukulu kuti wamng'anamuke Yesu kwa anyiiwo. 11Wakuluakulu wa ajhukulu yapo adavela nghani zimenezo, adakondwa, adamwahidi kumpacha ndalama. Ndiipo, yuda wadayamba kufunafuna malo ya kumng'anamuka Yesu.
Yesu wakudya chakudya cha Pasaka ni oyaluzidwa wake
Matayo 26:17-25; Luka 22:7-14,21-23; Yohana 13:21-30
12Pa siku loyamba la pwando la mabumunda yayo yalibe amila, ni siku la kumpha mwana wambelele wa Pasaka, oyaluzidwa wake adamfunjha, “Bwanji, ufuna tipite kuti tikukonjele pwando la Pasaka?”
13Yesu wadaatuma oyaluzidwa wake awili, wadaakambila, “Pitani kumujhi, kumeneko simummpheze wammuna mmojhi watenga mchuko. Mchateni mundhu mmeneyo, 14mbaka mnyumba iyo siwalowe, ndiipo mkamkambile mwene nyumba, ‘Oyaluza afunjha, bwanji, chili kuti chumba cha alendo kuti nidye chakudya cha Pasaka pamojhi ni oyaluzidwa wanga?’ 15Iye siwakulangizeni chumba chachikulu kugholofa icho chakonjekeledwa bwino ni kupambidwa. Tikonjekeleni mmenemo.”
16Oyaluzidwa adachoka, adapita kumujhi, adampeza kila chindhu chili ngati umo adakambilidwa ni Yesu. Adakonjekela chakudya cha Pasaka. 17Ujhulo yapo udajha, Yesu wadafika pa nyumba ijha pamojhi ni oyaluzidwa wake khumi ni awili. 18Yapo amadya, Yesu wadakambila, “Zenedi nikukambilani mmojhi pakati panu uyo wakudya niine, siwaning'anamuke.” 19Anyiwajha oyaluzidwa wake adayamba kudandaula, kila mmojhi wadamfunjha, “Bwanji, unikamba ine nde sinikung'anamuke?” 20Yesu wadaayangha, “Mmojhi wa anyiimwe khumi ni awili, uyo wasunjhila bumunda bakuli imohji ni ine. 21Ine mwana wa Mundhu sinimwalile ngati umo yalembedwela Malembo Yoyela. Nambho siwavutike mundhu yujha siwaning'anamuke ine mwana wa Mundhu, idakakhala mbasa mundhu mmeneyo siwadakabadwa!”
Chakudya cha Ambuye
Matayo 26:26-30; Luka 22:14-20; 1 Akolinso 11:23-25
22Yapo amadya, Yesu wadatenga bumunda, wadamuyamika Munungu, wadaubandhula ni kwapacha oyaluzidwa wake uku ni wakamba, “Tengani, mudye ili ni thupi langa.” 23Ndiipo wadatenga chikho cha divai, wadamuyamika Mnungu, wadaapacha, wonjhe adachimwela. 24Wadaakambila, “Uwu ni mwazi wanga uwo uchimikiza chipangano cha Mnungu, mwazi uwo umwazika ndande ya wandhu ambili. 25Zenedi ni kukambilani, sinimwa divai mbaka siku lijha yapo siniimwenjho divai yachipano ku Ufumu wa Mnungu.” 26Ndiipo adaimba nyimbo ya kumtamanda Mnungu yapo adamaliza kuimba, adachoka ni kupita ku phili la Mizeituni.
Yesu walosa kuti Petulo siwamkane
Matayo 26:31-35; Luka 22:31-34; Yohana 13:36-38
27Yapo adali mnjila Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, “Anyiimwe mwaonjhe simunithawe ni kunisiya ngati umo yalembedwela mmalembo Yoyela,
‘Mnungu siwambule owesa,
ni mbelele zonjhe sizimwazikane.’
28Nambho nikatho hyuka sinikuchogoleleni kupita ku Galilaya.” 29Chimwecho Petulo wadamkambila, “Ata ngati wonjhewa akakusiyani, nambho ine sinikusiyani.” 30Yesu wadamkambila Petulo, “Zene nikukambila, usiku wa lelo tambala wakali osalile mala kawili, siunikane mala katatu.” 31Nambho Petulo wadachimikiza kokamba, “Ata ngati ikafunika nife pamojhi ni imwe, sinikusiyani.” Niwajha oyaluzidwa wina nao adakamba chimwecho.
Yesu wapembhela mbusitani ya Getisemane
Matayo 26:35-46; Luka 22:39-46
32Adafika pamalo yapo pamatanidwa Getisemane. Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, “Khalani yapa ine yapo nipita kupembhela.” 33Ndiipo wadaatenga Petulo ni Yohana ni Yakobo, wadapita nao patali pang'ono, wadavela kupweteka mumtima ni kulaga. 34Wadaakambila, “Nili ni chisoni kupunda mumtima mwanga, chikhoza kunipha. Khalani yapa ni mchezelele.” 35Yesu wadapita pachogolo pang'ono, wadajhitaya panjhi chifufumimba, uku ni wapembha, “Ngati ikakhozekana sinidapitila saa iyi ya mavuto.” 36Wadapembha, “Atate wanga, kwanu vindhu vonjhe vikhozekana. Mnichochele chikho ichi cha mavuto, nambho isidakhala ngati umo nifunila ine, nambho ngati umo mfunila imwe.”
37Ndiipo yapo wadabwela wadaapheza oyaluzidwa wake atatu agona. Basi wadamfunjha Simoni uyo watanidwa Petulo, “Simoni wagona litulo? Siudakhoze kuchezelela ata saa imojhipe?” 38Ndiipo, wadaakambila, “Mchezelele ni mpembhele kuti simdayesedwa kuchita voipa. Anyiimwe mfuna kulimbila mtima mayeso nambho matupi yanu yalibe mbhavu.”
39Yesu wadapitanjho kupembhela uku niwakamba mawu yamweyajha. 40Ndiipo, wadaajhelanjho, ni wadaapheza agona, maso yao yadali ni litulo. Siadajhiwe cha kumuyangha.
41Yapo wadaajhela mala ya katatu wadaakambila, “Mkali kugona ni kupumulila? Ukani! Saa yathofika! Ine mwana wa Mundhu siniikidwe mmanja mwa wandhu amachimo. 42Nyakukani! Tijhipita! Mundhu uyo siwaning'anamuke wali pampano.”
Yesu wagwilidwa
Matayo 26:47-56; Luka 22:47-53; Yohana 18:3-12
43Yesu yapo wadali wakali kukamba, Yuda mmojhi wa anyiwajha oyaluzidwa khumi ni awili, wadafika. Wadajha pamojhi ni gulu la wandhu anyiawo adali ni maupanga ni vibonga. Adatumidwa ni wakulu wa ajhukulu ni oyaluza athauko ni achogoleli. 44Ndiipo Yuda yujha wadang'anamuka wadaapacha chizindikilo, wadaakambila, “Mundhu uyo sinimbusu nde mumfuna. Mgwileni ni kumuika pa ulonda, wasadathawa.”
45Pampajha Yuda yapo wadafika, wadamchata Yesu, ni wadamlonjela, “Oyaluza!” Ndiipo wadambusu. 46Ndiipo, wandhu wajha adamgwila Yesu ni kumuika panjhi pa ulonda. 47Nambho mmojhi wa wandhu waanyiwajha adaima pamojhi ni Yesu, wadasolomola upanga wake, wadamdula khutu mbowa wa mjhukulu wamkulu. 48Yesu wadaafunjha, “Bwanji, mwajha pano ni maupanga ni vibonga kunigwila ine ngati mnghungu? 49Kila siku nidali pamojhi ni anyiimwe uku niyaluza panyumba ya Mnungu, simdanigwile. Nambho yaya yachitika kuti Malembo Yoyela yakwanile.”
50Pamenepo oyaluzidwa wonjhe adamsiya ni kuthawa.
51Kudali ni mnyamata mmojhi wadavala shukape wamamchata Yesu. Yapo amafuna kumgwila, 52wadasiya shuka lake ni kuthawa popande kuvala.
Yesu pachogolo pa bwalo la milandu
Matayo 26:57-68; Luka 22:54-55,63-71; Yohana 18:13-14,19-24
53Ndiipo, adampeleka Yesu ku nyumba ya mjhukulu wa mkulu, pamenepo ajhukulu waakulu wonjhe, achogoleli ni oyaluza thauko adaphezana pamojhi. 54Petulo wamamchata Yesu kwa patali, wadalowa mseli ya mjhukulu wamkulu, wadakhala pamojhi ni alonda uku ni wamatoothela moto. 55Ajhukulu waakulu, ni wandhu wonjhe abwalo la milandu adafunafuna umboni wa kumpacha Yesu mlandu, kuti akhoze kumpha nambho siadaupate.
56Wandhu ambili adachocha umboni wa mthila kwa Yesu, nambho umboni wao siudalingane. 57Ndiipo wandhu wina adaima, ni kuchocha umboni wamthila niakamba, 58“Tidamvela mundhu uyu ni wakamba, ‘Sinigomole nyumba iyi ya Mnungu yamagwidwa kwa manja ya wandhu. Ni kwa masiku yatatu siniimange yina iyo siimangidwa kwa manja ya wandhu.’ ” 59Nambho ata chimwecho umboni wao siudalingane.
60Ndiipo, mjhukulu wamkulu wadaima pachogolo pa wandhu ni kumfujha Yesu, “Bwanji, siuyangha kandhu? Bwaji siuona kuti wandhu wonjhe yawa achocha umboni wa kukupacha mlandu iwe?” 61Nambho Yesu wadakhala chete, siwadakambe kandhu. Mjhukulu wamkulu wadamfunjhanjho, “Bwanji iwe nde Kilisito, Mwana wa Mnungu uyo watamandidwa?” 62Yesu wadamuyangha, “Nde ine. Ni anyiimwe simumuone ine mwana wa Mundhu nakhala janja la kwene la Mnungu wambhavu, ninijha mmitambo ya kumwamba.” 63Mjhukulu wamkulu wadang'amba njhalu zake kulangiza mbwayi ni kukamba, “Bwanji, tifunanjho amboni a chiyani? 64Mwachinawene mwavela umo wamkafulila Mnungu” Anyiimwe muona bwanji? Bwalo lonjhe lidamlamula waphedwe. 65Ndiipo wandhu wina adayamba kumlavulila Yesu malovu, adamcheka maso, adambula ni adamkambila, “Losa yani wakubula,” Chinchijha alonda nawo adamtenga ni kumbula.
Petulo wamkana Yesu
Matayo 26:69-75; Luka 22:56-62; Yohana 18:15-18,25-27
66Petulo yapo wadali wakali panjhi mseli, wamkazi mmojhi mbowa wa mjhukulu wamkulu wadajha. 67Yapo wadamuona Petulo ni waotha moto, wadampenyechecha, ni kumkambila, “Chimchijha iwe nawe udali pamojhi ni Yesu wa ku Nazaleti.” 68Nambho Petulo wadakana, “Sinimjhiwa ni sinichijhiwa icho uchikamba.” Ndiipo Petulo wadatuluka kubwalo mbaka kuseli. Pampajha tambala wadalila. 69Yujha mbowa yapo wadamwonanjho Petulo pamalo pajha, wadayamba kwaakambila wandhu wajha adaima pamenepo kuti, “Mundhu uyu nayo ni mmojhi wao.” 70Nambho Petulo wadakananjho.
Pambuyo pang'ono, wandhu wajha adaima pamenepo adampitila ni adamkambila Petulo, “Zenedi iwe ni mmojhi wao, pakuti iwe ni mundhu wa ku Galilaya.” 71Chimwecho Petulo wadayamba kujhileswa ni kujhilumbilila, “Ine sinijhiwa mundhu mmeneyo mumkamba nghani zake.” 72Pampajha tambala wadalila mala ya kawili. Ndiipo Petulo wadakumbukila umo Yesu wadamkambila, “Tambala wakali siwadalile mala kawili, siunikane mala katatu.” Chimwecho Petulo wadayamba kulila.

Àwon tá yàn lọ́wọ́lọ́wọ́ báyìí:

Maluko 14: NTNYBL2025

Ìsàmì-sí

Pín

Daako

None

Ṣé o fẹ́ fi àwọn ohun pàtàkì pamọ́ sórí gbogbo àwọn ẹ̀rọ rẹ? Wọlé pẹ̀lú àkántì tuntun tàbí wọlé pẹ̀lú àkántì tí tẹ́lẹ̀