1
Marko 1:35
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
Marko 1:15
“Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
3
Marko 1:10-11
Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda. Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”
4
Marko 1:8
Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”
5
Marko 1:17-18
Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
6
Marko 1:22
Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo.