Maluko 9
9
1Yesu wadayendekela kukamba, “Zenedi nikukambilani, pali wina pampano samwalila mbaka yapo sauone Ufumu wa Mnungu ni ujha kwa mbhavu.”
Yesu waoneka muulemelelo wake
Matayo 17:1-13; Luka 9:28-36
2Pambuyo pa masiku sita, Yesu wadaatenga Petulo ni Yakobo ni Yohana, wadapita nawo ku phili, kumalo kopande wandhu. Pamwepo Yesu wadang'anamuka nghope yake pamaso pawo, 3njhalu zake zidali zoyelambee, palibe mundhu pajhiko uyo wadakhoza kuzichapa ni kuhala zoyela mbee ngati zijha. 4Pampajha, oyaluzidwa atatu wajha wadaaona alosi Eliya ni Musa niakamba ni Yesu. 5Petulo wadamkambila Yesu, “Oyaluza, siikhale bwino ife tikhale pano. Chipano, timange visakasa vitatu, chimojhi chanu, chimojhi cha Musa, ni china cha Eliya.” 6Petulo siwadajhiwe chokamba ndande iye ni achanjake adaopa kupunda. 7Ndiipo udatulukila mtambo ni kwavinikila wonjhe, ni mvekelo wa Mnungu udaveka kuchokela mujha mumtambo, “Uyu ni mwana wanga wa mmuna uyo nimkonda, mvecheleni.” 8Pampajha yapo adapenya uku ni uku, siadamwone mundhu mwina pamojhi ni anyiiwo, nambho Yesu pe.
9Ndiipo, Yesu yapo amachika kuphili, wadaakaniza oyaluzidwa wake sadamkambila mundhu waliyonjhe vindhu ivo adaviona, mbaka yapo iye Mwana wa Mundhu siwahyuke. 10Adagwila lamulo lijha, nambho adajhifunjha, “Kuhyuka mate yake chiyani.” 11Oyaluzidwa wake adamfunjha Yesu, “Ndande yanji oyaluza athauko akamba ifunika Eliya wajhe uti wakali osajhe kilisito?” 12Yesu wadaayangha, “Yetu, Eliya wakujha uti kuika kilachindu bwino. Ata chimwecho, ndande yanji yalembedwa mmalembo yoyela kuti Mwana wa Mundhu wafunika kuvutika ni kudeleledwa? 13Nambho nikukambilani, Eliya wathokujha, ni anyiiwo adamchita icho amachifuna ngati umo yadalembedwela mmalembo yoyela.”#9:13 Eliya wathokujha, Yesu wadaalinganicha Yohana Mbatizi ni Eliya. Yohana Mbatizi wadachita njhito iyo Ayahudi amapenyelela, kuti Eliya siwaipote njhito yakumkonjela Yesu njila.
Yesu wamlamicha mnyamata wachiwanda
Matayo 17:14-21; Luka 9:37-43
14Yesu pamojhi ni oyaluzidwa wake atatu wajha, yapo adafika kwa oyaluzidwa wina adaliona gulu lalikulu la wandhu ni oyaluza athauko akumojhi amathochuchana nao. 15Pampajha, lijha gulu la wandhu lidaona, wonjhe adazizwa kupunda, ni adamthamangila ni kumlonjela. 16Yesu wadaafunjha oyaluzidwa wake, “Bwanji, mchuchana nao chiyani?” 17Mundhu mmojhi kuchokela mgulu la wandhu, wadamuyangha Yesu, “Oyaluza, nakupelekelani mwana wanga kwanu, wali ni chiwanda icho chamchita wakhale bubu. 18Ndhawi yaliyonjhe yapo chimzamwa chimtaya panjhi ni kumchita wachoke ni matovu mkamwa, ni kutafuna mano yake, ni watouma thupi lake. Nidaapembha oyaluzidwa wako amchoche chiwanda chimenecho, nambho siadakhoze.”
19Yesu wadaakambila, “Anyiimwe mbadwa ulibe chikhulupililo, sinikhale ni anyiimwe mbaka siku liti? Sinikulimbileni mtima mbaka siku lanji? Majhanayoni pano mwana mmeneyo.” 20Chimwecho adampeleka kwa Yesu yujha wadali ni chiwanda.
Pampajha, chijha chiwanda yapo chidamwona Yesu, chidamchita wakhale ni njili, wadangwa panjhi, wadawalauka ni kuchocha matovu mkamwa. 21Yesu wadamfunjha tate wayujha mwana, “Bwanji, utenda uwu wampata kuyambila siku lanji?” wadamuyangha, “Kuyambila yapo wadali mwana. 22Ninyengo za mbili chiwanda chimenecho chimgwecha pamoto ni pamajhi, kuti chimphe. Nambho, ngati mkhoza kuchita chindhu, tilengele lisungu, utithangatile!” 23Yesu wadamkambila, “Ngati uli ni chikhulupililo, yonjhe yakhozeka kwa uyo wakhulupilila.” 24Pampajha, tate wa yujha mwana wadalila kwa mvekelo, “Nikhulupilila! Nambho chikhulupililo changa chaching'ono, nithangatileni kuti nikhoze kukhulupilila.”
25Yesu yapo wadaona gulu la wandhu lichuluka kwa chisanga, wadachinyindila chijha chiwanda, “Iwe chiwanda umchita uyu mundhu kukhala wosakamba ni wosavela, nikulamula mchoke mnyamata uyu ni siudamlowanjho!” 26Pampajha, chijha chiwanda chidatutuma ni kumgwecha njili ni kumchoka. Mwana yujha wadaoneka ngati wamwalila, ni wandhu ambili adakamba, “Wathomwalila!” 27Nambho Yesu wadamgwila jhanja mnyamata yujha, wadamthangatila kunyakuka, nayo wadanyakuka.
28Ndiipo, Yesu yapo wadalowa mnyumba, oyaluzidwa wake adamfunjha paokha, “Ndande yanji ife sitidakhoze kumchocha chiwanda chijha?” 29Yesu wadaakambila, “Chiwanda ngati ichi sichikoza kuchoka, ingakhale kwa kupembhelape.”
Yesu wakambanjho nghani za nyifa yake
Matayo 17:22-23; Luka 9:43-45
30Yesu ni oyaluzidwa wake adachoka pamenepo, adayendekela ni ulendo kopitila Galilaya. Yesu siwadafune mundhu waliyonjhe wajhiwe uko wali, 31ndande wamatowayaluza oyaluzidwa wake. Wadaakambila, “Ine Mwana wa Mundhu sinikidwe mmanja mwa wandhu, ni nawo sianimphe, siku la katatu sinihyuke.” 32Nambho oyaluzidwa wake siadajhiwe mate ya mawu yameneyo, ni adaopa kumfunjha.
Yani uyo wali niukulu?
Matayo 18:1-5; Luka 9:46-48
33Yesu ni oyaluzidwa wake yapo adafika kumujhi wa Kapelinaumu, adalowa mkati, ni Yesu wadaafunjha oyaluzidwa wake, “Yapo mdali mnjila mmachuchanilana chiyani?” 34Nambho anyiiwo sadamuyanghe, pakuti amachuchana yani wali niukulu pakati pao.
35Yesu wadakhala panjhi, ni wadaatana anyiwajha oyaluzidwa wake khumi ni awili ni kwakambila, “Mundhu waliyonjhe wakafuna kukhala woyamba, ifunika wakhale wothela ni wakhale mbowa wa wandhu wonjhe.” 36Ndiipo, wadamtenga mwana wamng'ono, ni kumwimika pakati pao, wadamvumbatila ni kwakambila, 37“Mundhu waliyonjhe uyo wamlandila mwana wamng'ono ngati uyu ndande yaine wanilandila ine, ni siwanilandila inepe, chinchijha wamlandila Mnungu uyo wanituma.”
Mundhu uyo siwachuchana ni ife wali pamojhi ni ife
Luka 9:49-50
38Yahana wadamkambila Yesu, “Oyaluza tamuona mundhu mmojhi ni wachocha chiwanda kwa jhila lanu, tamkaniza ndande siwachoka mgulu lathu.” 39Yesu wadaakambila, “Simdamkaniza mundhu waliyonjhe wachita vodabwicha mwajhina langa. Pamwepo wanikambe kuipa. 40Mundhu uyo siwachuchana ni ife, wali pamojhi ni ife. 41Zenedi nikukambilani, mundhu waliyonjhe uyo siwakupacheni chikho cha majhi ya kumwa, ndande ya anyiimwe ni wandhu wake Kilisito, mundhu mmeneyo siwalandile mbhaso yake.”
Vindhu ivo vimchiticha mundhu wachite machimo
Matayo 18:6-9; Luka 17:1-2
42“Mundhu waliyonhje uyo siwamchitiche wana yawa anikhulupilila ine achite machimo, idakakhala bwino mundhu mmeneyo wamangwidwe mbhelo ya ikulu pakhosi ni kutaidwa mnyanja yamchele. 43Ngati jhanja lako likakuchiticha uchite machimo, lidule! Mbasa kulowa mu umoyo wa muyaya popande jhanja limojhi, kusiyana kukhala ni manja yawili ni kulowa mmoto wa muyaya. 44Mmenemo muli mafuchi yayo siyakufa, ni moto uwaka muyaya. Bibiliya zina za kale zilibe mzele uwu. Chimchijha chindhu ichi balibenjho pa mzele wa 48. 45Ni mwendo wako ukakuchiticha uchite machimo, udule! Mbasa kulowa mu umoyo wa muyaya ulibe myendo umojhi, kusiyana ni kukhala ni myendo iwili ni kutaidwa mumoto wa muyaya. 46Mmenemo muli mafuchi yayo siyakufa, ni moto wa muyaya. 47Ni diso lako likakuchiticha uchite machimo, lizule, mbasa kulowa mu umoyo wa muyaya uku uli ni diso limojhipe, kusiyana kukhala ni maso yonjhe yawili ni kutaidwa mumoto wa muyaya. 48Mmenemo muli mafuchi yayo siyakufa, ni moto uwo uwaka muyaya.”
49“Mnungu siwampitiche kila mundhu pamavuto yayo yali ngati moto, ni ngati umo wandhu atila mchele mnyama ikali yosabuchidwe. 50Mchele ni wabwino, nambho ngati ukataiza kukoma kwake, siuthilidwe chiyani kuti ukomenjho? Mkhale ngati mchele uwo ukoma, ni mkhale kwa mtendele ni achanjanu.”
നിലവിൽ തിരഞ്ഞെടുത്തിരിക്കുന്നു:
Maluko 9: NTNYBL2025
ഹൈലൈറ്റ് ചെയ്യുക
പങ്ക് വെക്കു
പകർത്തുക

നിങ്ങളുടെ എല്ലാ ഉപകരണങ്ങളിലും ഹൈലൈറ്റുകൾ സംരക്ഷിക്കാൻ ആഗ്രഹിക്കുന്നുണ്ടോ? സൈൻ അപ്പ് ചെയ്യുക അല്ലെങ്കിൽ സൈൻ ഇൻ ചെയ്യുക
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: