Maluko 8
8
Yesu waapacha chakudya wandhu elufu zinayi
Matayo 15:32-39
1Pa masiku yameneyo, gulu lalikulu la wandhu lidapezananjho, ni adalibe chakudya. Ndiipo, Yesu wadaatana oyaluzidwa wake, ni kwakambila, 2“Nialengela lisungu wandhu anyiawa, ndande akhala niine masiku yatatu ni alibe chindhu cha kudya. 3Nikaasiya abwele mmakhomo yao uku ali ni njala, siakomoke mnjila ndande wina achokela kutali.”
4Oyaluzidwa wake adamfunjha, “Pano ni paphululu, sitipate kuti chakudya cha kwaapacha wandhu wonjhewa?” 5Yesu wadaafunjha, “Muli ni mabumunda yangati?” Adamuyangha, “Tili ni mabumunda saba.”
6Yesu wadaakambila wandhu akhale panjhi. Wadayatenga yajha mabumunda saba, wadamuyamika Mnungu, wadaibandhula ni kwapacha oyaluzidwa wake wagawile wandhu, nawo oyaluzidwa wake adachita chimwecho. 7Chimwechonjho adali ni njhomba zazing'onozing'ono zochepa. Yesu wadamuyamika Mnungu, ni chinchijha wadaakambila oyaluzidwa wake wagawile wandhu. 8Wandhu adadya ni kukhuta. Ndiipo woyaluzidwa wake adakusa vakudya vidakhalila ni kujhaza miseche saba. 9Ni wandhu yawo adadya adali ngati elufu zinayi. Ndiipo Yesu wadaalaila wandhu apite kumakomo yao, 10pampajha wadakwela mboti pamojhi ni oyaluzidwa wake, wadapita kumujhi wa Dalimanuta.
Afalisayo afuna vizindikilo
Matayo 16:1-4
11Afalisayo akumojhi adamchata Yesu ni kuyamba kumfunjha kwa kumuyesa ni kufuna chizindikilo cholangiza kuti iye wachokela kumwamba. 12Nambho Yesu wadadandaula mumtima mwake, wadakamba, “Ndande yanji mbadwa uwu ufuna chizindikilo? Zenedi nikukambilani, mbadwa uwu siulangizidwa chizindikilo chilinjhonjhe.” 13Ndiipo, Yesu wadaasiya Afalisayo, wadakwelanjho pamojhi ni oyaluzidwa wake mboti, ni kuyomboka kuchijya.
Amila ya Afalisayo ni Helode
Matayo 16:5-12
14Oyaluzidwa wake adayawalila kutenga mabumunda yokwana, adali ni bumunda limojhipe mbwato. 15Yesu wadataazalicha oyaluzidwa wake, wadaakambila, “Mkhale maso ni amila ya afalisayo ni amila ya Helode.” 16Oyaluzidwa wake adayamba kukambilana, “Wakamba chimwechi ndande tilibe mabumunda.” 17Yesu wadajhiwa icho amakambilina, wadaafunjha, “Ndande yanji, mchuchana ndande mulibe mabumunda? Bwanji, mkali osajhiwe kapina kuzindikila? Bwanji, mitima yanu ikali yolimba? 18Bwanji, muli ni maso nambho simpenya, ni muli ni makutu nambho simvela? Bwanji, simkumbukila 19ndhawi ijha nidabandhula mabumunda yasano, ni kwapacha wandhu elufu zisano? Bwanji, mdajhaza miseche ingati ya mabumunda yayo yadakhalila?” Adayangha, “Miseche khumi ni iwili.” 20“Niyapo nidayabandhula yajha mabumunda saba nikwapacha wandhu elufu zinayi, mdatondola miseche ingati ya mabumunda iyo idakhalila?” Adayangha, “Miseche saba.” 21Ndiipo wadaafunjha, “Bwanji, mkali simjhiwa?”
Yesu wamlamicha mundhu wosapenya ku Betisaida
22Yesu ni oyaluzidwa wake adafika kumujhi wa Betisaida, wandhu adampelekela mundhu uyo siwamapenye, adampembha kupunda wamgafye kuti wamlamiche. 23Yesu wadamgwila yujha mundhu jhanja, ni kumtulucha kubwalo kwa mujhi. Ndiipo wadamlavulila malovu mmaso, wadamuikila manja ni kumfunjha “Bwanji, uona chiyani?” 24Yujha mundhu wadapenya ni kukamba, “Niona wandhu ali ngati mitengo niayenda.” 25Ndiipo, Yesu wadamuikilanjho manja mmaso, ni maso yake yadamasuka, wadaona bwino kilakandhu. 26Yesu wadamkambila wabwele kukhomo lake ni kumlamula, “Siudalowa mkati mmujhi!”
Petulo wachimikiza kuti Yesu ni Kilisito
Matayo 16:13-20; Luka 9:18-21
27Ndiipo, Yesu ni oyaluzidwa wake adapita ku vijhijhi va Kaisalia Filipi. Mnjila Yesu wadaafunjha oyaluzidwa wake, “Bwanji, wandhu akamba kuti ine ni yani?” 28Adamuyangha, “Wina akamba kuti iwe ni Yohana Mbatizi, wina akamba kuti iwe ni mlosi Eliya, ni wina akamba kuti iwe ni mmojhi wa alosi wina.” 29Ndiipo Yesu wadaafunjha, “Bwanji, anyiimwe mkamba kuti ine ni yani?” Petulo wadamuyangha, “Iwe nde Kilisito.” 30Ndiipo, Yesu wadaakaniza oyaluzidwa wake, “Msadamkambila mundhu waliyonjhe nghani zakuti ine ni Kilisito.”
Yesu walosa mavuto ni nyifa yake
Matayo 16:21-28; Luka 9:22-27
31Ndiipo, Yesu wadayamba kwayaluza oyaluzidwa wake, “Ine mwana wa Mundhu nifunika nivutike kupunda, ni kukanidwa ni azee ni wakuluakulu waajhukulu ni oyaluza athauko la musa. Ni wafunika waphedwe, ni wahyuke siku la katatu.” 32Yesu wadaakambila mawu limenelo popande kwaabisa. Pamenepo, Petulo wadamtenga Yesu pambhepete, ni kuyamba kumnyindila. 33Nambho Yesu wadang'anamuka, wadaapenya oyaluzidwa wake, ni kumtutumila Petulo, “Bwela kumbuyo kwanga iwe Satana! Ndande maganizo yako siyachokela kwa Mnungu, nambho yachokela kwa wandhu.”
34Ndiipo Yesu wadalitana gulu la wandhu pamojhi ni oyaluzidwa wake, wadaakambila, “Mundhu waliyonjhe wafuna kunichata ine, ifunika wajhikane mwene wake, wavomele kuvutika mbaka kufa ni wanichate ine. 35Pakuti mundhu uyo wafuna kuuombola umoyo wake, siwautaize, nambho mundhu uyo siwautaize umoyo wake ndande yanga ni kwa ndande ya Uthenga Wabwino, siwauombole. 36Bwanji, mundhu siwapate phindu lanji wakavipata vindhu vonjhe vapajhiko, nambho wakautaiza umoyo wake? 37Mundhu siwachoche chiyani kuti wakhoze kuombola umoyo wake? 38Mundhu waliyonjhe uyo wanionela njhoni ine ni Uthenga Wabwino pa mbadwa wachipano uwo wakana kumjhiwa Mnungu ni kuchita voipa, ine Mwana wa Mundhu nane sinimkane mundhu mmeneyo, yapo sinijhe pa ulemelelo wa Atate wanga ni wa atumiki oyela akumwamba.”
നിലവിൽ തിരഞ്ഞെടുത്തിരിക്കുന്നു:
Maluko 8: NTNYBL2025
ഹൈലൈറ്റ് ചെയ്യുക
പങ്ക് വെക്കു
പകർത്തുക

നിങ്ങളുടെ എല്ലാ ഉപകരണങ്ങളിലും ഹൈലൈറ്റുകൾ സംരക്ഷിക്കാൻ ആഗ്രഹിക്കുന്നുണ്ടോ? സൈൻ അപ്പ് ചെയ്യുക അല്ലെങ്കിൽ സൈൻ ഇൻ ചെയ്യുക
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.