Maluko 7
7
Mayaluzo kuusu chikhalidwe cha azee
Matayo 15:1-9
1Siku limojhi, Afalisayo ni woyaluza akumojhi athauko yawo adachokela ku Yelusalemu, adasonghana pachogolo pa Yesu. 2Adaaona akumojhi awoyaluzidwa wake niadya chakudya kwa manja najhisi, pakuti siadasambe bwino manja yawo ngati umo khalidwe la azee limafunila. 3Pakuti Afalisayo ni Ayahudi ni wandhu wina wonjhe achata makhalidwe ya azee wao. Siakudya popande kusamba mbaka mvigwinghwi va mmanja. 4Niakachoka ku soko kugula chindhu, siakudya mbaka asambe. Chinchijha adagwila vikhalidwe vina, ngati vochuka vikombe, miphika ni mbale zodyela.
5Ndiipo Afalisayo ni oyeluza athauko la Musa adamfunjha Yesu, “Ndande yanji oyaluzidwa wako siachata makhalidwe yayo talandila kuchokela kwa azee wathu, nambho anyiiwo akudya popande kusamba mbaka mvigwinghwi va mmanja?” 6Yesu wadaayangha, “Agunghuli anyiimwe, mlosi Isaya wadakuloselani bwino anyiimwe, yapo wadalemba,
‘Mnungu wakamba, wandhu anyiawa anilimekeza kwa milomo yaope,
nambho mitima yao, ilikutali niine.
7Ni kunilambila kwawo sikufunika,
pakuti ayaluza mayaluzo ya wandhupe ngati mayaluzo ya Mnungu.’”
8“Anyiimwe muyasiya malamulo ya Mnungu ni kuchata chikhalidwe cha wandhu.”
9Yesu wadaendekela kukamba, “Anyiimwe mkana mayaluzo ya Mnungu ni kuchata chikhalidwe chanu. 10Musa wadaagiza, ‘Alemekeze amako ni atate wako,’ ni ‘Mundhu uyo siwaatukane atate wake kapina amake siwafe.’ 11Nambho anyiimwe muyaluza ngati mundhu uyo wali ni chindhu chakwaathangatila atate wake ni amake, nambho mkamba, ‘Thandizo ilo nidakupachani ni Kolobani’ mate yake chindhu ichi chapatulidwa ndande ya kumchochela Mnungu, 12kwakuyaluza chimwecho mwachekeleza wandhu, siwadathangatila atate wao kapina amao. 13Chimwecho, ndeumo mulidelela mawu la Mnungu ndande ya makhalidwe yanu yayo mudayalandila. Ni mchita vindhu vambili va mtundu umeneo.”
Vindhu ivo vimchita mundhu siwadavomelezeka kwa Mnungu
Matayo 15:10-20
14Yesu wadalitananjho lijha gulu la wandhu, ni kulikambila, “Mnivechele mwaonjhe kuti mjhiwe. 15Palibe chindhu chilowa mkati mwa mundhu kuchokela kubwalo icho chikhoza kumchita siwadavomelezeka kwa kumlambila Mnungu. Nambho icho chichoka mkati mwa mundhu ndeicho chimchita mundhu siwadavomelezeka kwa kumlambila Mnungu. 16Mchate yayo mkambidwa!”#7:16 Bibilia zina zakale zilibe mzele uwu
17Yesu yapo wadalisiya gulu la wandhu ni kulowa mkati, oyaluzidwa wake adamfunjha mate ya ujha mkuluwiko. 18Yesu wadaakambila, “Bwanji, nianyiimwe namwenjho simjhiwa? Bwanji, simjhiwa kuti icho chimlowa mundhu kuchokela kubwalo, sichikoza kumchita mundhu wakanidwe kumlambila Mnungu? 19Pakuti sichilowa mumtima, nambho chilowa mmimba, ni pambuyo chituluka kubwalo kwa thupi lake ni kupita kudambo.” Kwakukamba chimwecho, Yesu wadavichita vakudya vonjhe vivomelezeke kudyedwa.
20Wadaendekela kukamba, “Icho chichoka mkati mwa mundhu nde chimchita mundhu siwadavomelezeka kumlambila Mnungu. 21Pakuti kuchokela mmitima ya wandhu, yachoka maganizo yoipa ni chigololo ni unghungu ni kupha, 22uhule ni khumbilo lo funa chuma chambili ni voipa ni unami ni kukafula ni khumbilo lofuna chigololo ni mbwinya ni usabwabwa. 23Voipa vimenevo vichoka mkati mwa wandhu, navo vimchita mundhu siwadavomelezeka kumlambila Mnungu.”
Chikhulupililo cha wamkazi mmojhi uyo siwadali Muyahudi
Matayo 15:21-28
24Yesu wadachoka pamenepo, nikupita ku mujhi wa Tilo. Kumeneko wadalowa mnyumba imojhi ni siwadafune mundhu wajhiwe, nambho siwadakhoze kujhibisa. 25Pajha padalipo ni wamkazi mmojhi uyo wadali ni mwali wa chiwanda, yapo wadavela kuti Yesu wali pajha. Wadajha ni kugwada, pachogolo pa myendo ya Yesu. 26Yapo wadamgwadila wadampembha Yesu wamchoche chiwanda mwali wake, nambho wamkazi mmeneyo wadali osati Muyahudi, uyo wadabadwila ku Foinike mjhiko la Siliya. 27Yesu wadamkambila, “Asiye wana akhute uti. Pakuti osati bwino kutenga chakudya cha wana ni kwaponyela agalu.”
28Nambho yujha wamkazi wadamyangha, “Ambuye ni chazene icho mwakamba, nambho ata agalu ali panjhi pa meza akudya vakudya ivo vikhalila kwa wana.”
29Yesu wadamkambila wamkazi yujha, “Ndande wayangha bwino, pita kukhomo kwako ni siumpheze mwali wako walama ni chiwanda chamchoka!”
30Chimwecho wamkazi yujha wadapita kukhomo lake, wadampheza mwana wake wagona pachika, ni chiwanda chathomchoka.
Yesu wamlamicha bubu gondhi
31Wadachoka mmujhi wa Tilo ni kupita ku Sidoni mbaka ku nyanja ya Galilaya ni kufika pamalo pa Dekapoli, mate yake mijhi khumi. 32Kumeneko, wandhu adampelekela bubu gondhi kwa Yesu, ni adampembha kupunda wamuikile manja kuti wamlamiche. 33Yesu wadamchocha yujha bubu gondhi kumbhepete kwa wandhu ni wadamuikila vyala mmakutu, wadalavula malovu ni kuligafya lilime la yujha mundhu. 34Wadapenya kumwamba, wadapuma kwa mbhavu ni kumkambila, “Efata” mate yake, “Masuka.” 35Pampajha, makutu yake yadamasuka, ni lilime lake nalo lidalenda, wadayamba kukamba bwino. 36Ndiipo Yesu wadaalamula asadamkambila mundhu waliyonjhe nghani zijha. Nambho umo wadapunda kwaakanizila, nde umo adayendekela kuziyeneza zijha nghani. 37Wandhu adazizwa kupunda nikukamba, “Wavichita ivi vonjhe bwino, wamkhozecha agondhi kuvela, ni mabubu akambe!”
നിലവിൽ തിരഞ്ഞെടുത്തിരിക്കുന്നു:
Maluko 7: NTNYBL2025
ഹൈലൈറ്റ് ചെയ്യുക
പങ്ക് വെക്കു
പകർത്തുക

നിങ്ങളുടെ എല്ലാ ഉപകരണങ്ങളിലും ഹൈലൈറ്റുകൾ സംരക്ഷിക്കാൻ ആഗ്രഹിക്കുന്നുണ്ടോ? സൈൻ അപ്പ് ചെയ്യുക അല്ലെങ്കിൽ സൈൻ ഇൻ ചെയ്യുക
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: