MALAKI 4

4
Oipa adzalangidwa, okoma adzadalitsidwa. Asamale chilamulo; adzafika Eliya
1 # Yow. 2.31 Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi. 2#Luk. 1.78; Aef. 5.14Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola. 3Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.
4 # Eks. 20.3-17; Deut. 4.10 Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho m'Horebu chikhale cha Israele lonse, ndicho malemba ndi maweruzo. 5#Yow. 2.31; Mat. 11.13-14; 17.11Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. 6#Zek. 14.12Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.

നിലവിൽ തിരഞ്ഞെടുത്തിരിക്കുന്നു:

MALAKI 4: BLPB2014

ഹൈലൈറ്റ് ചെയ്യുക

പങ്ക് വെക്കു

പകർത്തുക

None

നിങ്ങളുടെ എല്ലാ ഉപകരണങ്ങളിലും ഹൈലൈറ്റുകൾ സംരക്ഷിക്കാൻ ആഗ്രഹിക്കുന്നുണ്ടോ? സൈൻ അപ്പ് ചെയ്യുക അല്ലെങ്കിൽ സൈൻ ഇൻ ചെയ്യുക