1
MARKO 4:39-40
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu. Ndipo ananena nao, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi?
Konpare
Eksplore MARKO 4:39-40
2
MARKO 4:41
Ndipo iwo anachita mantha akulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
Eksplore MARKO 4:41
3
MARKO 4:38
Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?
Eksplore MARKO 4:38
4
MARKO 4:24
Ndipo ananena nao, Yang'anirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu.
Eksplore MARKO 4:24
5
MARKO 4:26-27
Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka; nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira.
Eksplore MARKO 4:26-27
6
MARKO 4:23
Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve.
Eksplore MARKO 4:23
Akèy
Bib
Plan yo
Videyo