1
Mateyu 27:46
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Ndipo nthawi ili ngati 3 koloko, Yesu analira mofuwula nati, “Eloi, Eloi, lama sabakitani!” Kutanthauza kuti, “Mulungu Wanga, Mulungu Wanga, mwandisiyiranji Ine?”
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
Mateyu 27:51-52
Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika. Manda anatsekuka ndipo mitembo yambiri ya anthu oyera mtima amene anafa inaukitsidwa.
3
Mateyu 27:50
Ndipo pamene Yesu analiranso mofuwula, anapereka mzimu wake.
4
Mateyu 27:54
Mkulu wa asilikali ndi amene ankalondera Yesu ataona chivomerezi ndi zonse zinachitika, anachita mantha, ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu!”
5
Mateyu 27:45
Kuyambira 12 koloko masana mpaka 3 koloko, kunachita mdima pa dziko lonse.
6
Mateyu 27:22-23
Pilato anafunsa kuti, “Nanga ndichite chiyani ndi Yesu wotchedwa Khristu?” Onse anayankha kuti “Mpachikeni!” Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wachita choyipa chotani?” Koma anachita phokoso nafuwula kwambiri kuti, “Mpachikeni!”