1
Mateyu 21:22
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
Mateyu 21:21
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi.
3
Mateyu 21:9
Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti, “Hosana Mwana wa Davide!” “Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!” “Hosana mmwambamwamba!”
4
Mateyu 21:13
Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.”
5
Mateyu 21:5
“Uza mwana wamkazi wa Ziyoni, taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yofatsa ndi yokwera pa bulu, pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.”
6
Mateyu 21:42
Yesu anawawuza kuti, “Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti: “ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana, womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya. Ambuye wachita izi, ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’
7
Mateyu 21:43
“Nʼchifukwa chake ndi kukuwuzani kuti ufumu wa Mulungu udzalandidwa kwa inu ndipo udzapatsidwa kwa anthu amene adzabereka chipatso chake.