1
Mateyu 18:20
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo.”
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
Mateyu 18:19
“Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani.
3
Mateyu 18:2-3
Iye anayitana kamwana kakangʼono ndi kukayimiritsa pakati pawo. Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba.
4
Mateyu 18:4
Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba.
5
Mateyu 18:5
Ndipo aliyense amene alandira kamwana kakangʼono ngati aka mu dzina langa, alandira Ine.
6
Mateyu 18:18
“Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba.
7
Mateyu 18:35
“Umu ndi mmene Atate anga akumwamba adzachitira ndi aliyense wa inu ngati simukhululukira mʼbale wanu ndi mtima wonse.”
8
Mateyu 18:6
“Koma ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana awa, amene akhulupirira Ine, kuti achimwe, kukanakhala bwino kuti iye amangiriridwe chimwala chachikulu mʼkhosi mwake ndi kumizidwa pansi pa nyanja.
9
Mateyu 18:12
“Kodi mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi nʼkusowa, kodi sasiya 99 zija mʼmapiri ndi kupita kukafuna imodzi yosocherayo?