1
Mateyu 15:18-19
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Koma zinthu zimene zituluka mʼkamwa zimachokera mu mtima ndipo zimenezi zimamuchititsa munthu kukhala woyipa. Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
Mateyu 15:11
Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu sichimuchititsa kukhala woyipa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake, icho ndi chimene chimamuchititsa kukhala woyipa.”
3
Mateyu 15:8-9
“ ‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine. Amandilambira Ine kwachabe ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’ ”
4
Mateyu 15:28
Pomwepo Yesu anayankha kuti, “Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka.” Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.
5
Mateyu 15:25-27
Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, “Ambuye ndithandizeni!” Iye anayankha kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu.” Mayiyo anati, “Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo.”