1
Mateyu 11:28
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.
Yenzanisa
Ongorora {{vhesi}}
2
Mateyu 11:29
Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
3
Mateyu 11:30
Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”
4
Mateyu 11:27
“Zinthu zonse zapatsidwa kwa Ine ndi Atate anga. Palibe mmodzi amene adziwa Mwana kupatula Atate ndipo palibe mmodzi amene adziwa Atate kupatula Mwana ndi kwa iwo amene Mwana awasankha kuwawululira.
5
Mateyu 11:4-5
Yesu anayankha kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwamva ndi kuona. Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka.
6
Mateyu 11:15
Iye amene ali ndi makutu amve.