EKSODO 12:12-13
EKSODO 12:12-13 BLPB2014
Pakuti ndidzapita pakati pa dziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova. Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.


