1
Lk. 13:24
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
“Yesetsani kuloŵera pa khomo lophaphatiza, pakuti kunena zoona anthu ambiri adzafuna kuloŵa, koma adzalephera.
ತಾಳೆಮಾಡಿ
Lk. 13:24 ಅನ್ವೇಷಿಸಿ
2
Lk. 13:11-12
M'menemo munali mai wina amene anali ndi mzimu woipa umene udamudwalitsa zaka 18. Anali ndi msana wokhota, mwakuti sankatha konse kuŵeramuka. Pamene Yesu adamuwona, adamuitana namuuza kuti, “Mai inu, mwamasuka ku matenda anu.”
Lk. 13:11-12 ಅನ್ವೇಷಿಸಿ
3
Lk. 13:13
Adamsanjika manja, ndipo pompo maiyo adaongoka, nayamba kutamanda Mulungu.
Lk. 13:13 ಅನ್ವೇಷಿಸಿ
4
Lk. 13:30
Pamenepo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira, ndipo amene ali oyambirira adzakhala otsirizira.”
Lk. 13:30 ಅನ್ವೇಷಿಸಿ
5
Lk. 13:25
“Mwini nyumba adzanyamuka nkutseka pa khomo. Pamenepo, okhala panjanu mudzayamba kugogoda nkumanena kuti, ‘Ambuye, titsekulireni.’ Koma Iye adzakuyankhani kuti, ‘Sindikudziŵa kumene mukuchokera.’
Lk. 13:25 ಅನ್ವೇಷಿಸಿ
6
Lk. 13:5
Iyai, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja.”
Lk. 13:5 ಅನ್ವೇಷಿಸಿ
7
Lk. 13:27
Koma Iye adzakuuzani kuti, ‘Pepani, sindikudziŵa kumene mukuchokera. Chokani apa nonsenu, anthu ochita zoipa.’
Lk. 13:27 ಅನ್ವೇಷಿಸಿ
8
Lk. 13:18-19
Yesu adati, “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, ndipo ndingauyerekeze ndi chiyani? Uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m'munda mwake. Idamera nisanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.”
Lk. 13:18-19 ಅನ್ವೇಷಿಸಿ
ಮುಖಪುಟ
ಬೈಬಲ್
ಯೋಜನೆಗಳು
ವೀಡಿಯೊಗಳು