Mt. 2:1-2
Mt. 2:1-2 BLY-DC
Yesu adabadwira m'mudzi wa Betelehemu, m'dziko la Yudeya, pa nthaŵi imene Herode anali mfumu ya dzikolo. Ndiye kudaabwera akatswiri ena a nyenyezi ku Yerusalemu kuchokera kuvuma. Iwowo ankafunsa kuti, “Ali kuti mwana amene adabadwa kuti adzakhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.”


