YouVersion Logo
Search Icon

NAHUMU 3

3
Zoipa za Ninive ndi kupasuka kwake
1 # Hab. 2.12 Tsoka mudzi wa mwazi! Udzala nao mabodza ndi zachifwamba; zachifwamba sizidukiza. 2Kumveka kwa chikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magaleta; ndi kaphatakaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magaleta; 3munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong'anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi chimulu cha mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda; 4chifukwa cha chiwerewere chochuluka cha wachiwerewere wokongola, ndiye mkaziyo mwini nyanga, wakugulitsa amitundu mwa chiwerewere chake, ndi mabanja mwa nyanga zake. 5#Nah. 2.13Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsalu yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umaliseche wako, ndi mafumu manyazi ako. 6#Mala. 2.9Ndipo ndidzakuponyera zonyansa, ndi kukuchititsa manyazi, ndi kukuika chopenyapo. 7#Chiv. 18.10Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthawa, nadzati, Ninive wapasuka, adzamlira maliro ndani? Ndidzakufunira kuti akukutonthoza? 8#Yer. 46.25Kodi uli wabwino woposa No-Amoni, wokhala pakati pa mitsinje wozingidwa ndi madzi; amene tchemba lake ndilo nyanja, ndi linga lake ndilo nyanja? 9Kusi ndi Ejipito ndiwo mphamvu yake, ndiyo yosatha, Puti ndi Libiya ndiwo akukuthandiza. 10#Yes. 13.16Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ake a makanda anaphwanyika polekeza pake pa miseu yake yonse; ndi pa omveka ake anachita maere, ndi akulu ake onse anamangidwa maunyolo. 11Iwenso udzaledzera, udzabisala; iwenso udzafunanso polimbikira chifukwa cha mdani. 12#Chiv. 6.13Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akagwedeza zingokugwa m'kamwa mwa wakudya. 13#Yer. 50.37Taona, anthu ako m'kati mwako akunga akazi, zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakulu; moto watha mipingiridzo yako. 14Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa. 15#Yow. 1.4, 6Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati chirimamine; udzichulukitse ngati chirimamine, udzichulukitse ngati dzombe. 16Wachulukitsa amalonda ako koposa nyenyezi za kuthambo; chirimamine anyambita, nauluka, nathawa. 17#Chiv. 9.7Ovala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazemba ako ngati ziwalamsatsi zakutera m'matchinga tsiku lachisanu, koma likafundukula dzuwa ziuluka nizithawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso. 18#Mas. 76.6Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asiriya; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa. 19#Mik. 1.9; Zef. 2.15Palibe chakulunzitsa kuthyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?

Currently Selected:

NAHUMU 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in