Malaki 3:11-12
Malaki 3:11-12 CCL
Ndidzaletsa tizirombo kuti tisawononge mbewu zanu, ndipo mpesa wa mʼminda mwanu zipatso zake sizidzayoyoka,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Motero anthu amitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.





