YouVersion Logo
Search Icon

YOHANE 1

1
Umulungu wa Yesu Khristu
(Aheb. 1.5-13)
1 # Akol. 1.17; Yoh. 17.5; Afi. 2.6 Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu. 2#Afi. 2.6Awa anali pachiyambi kwa Mulungu. 3#Akol. 1.16Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwe kanthu kalikonse kolengedwa. 4#Yoh. 5.26; Yoh. 8.12Mwa Iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu. 5#Yoh. 3.19Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikire.
Utumiki wa Yohane Mbatizi
(Mat. 3.1-17; Mrk. 1.1-11; Luk. 3.1-23; Yoh. 1.29-34)
6 # Mala. 3.1 Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake ndiye Yohane. 7#Mac. 19.4Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye. 8Iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukachita umboni wa kuunikaku.
Yesu Khristu kuunika koona kutifikira mwa kubadwa m'thupi
9 # Yes. 49.6 Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi. 10#Yoh. 16.3Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi Iye, koma dziko silinamzindikira Iye. 11#Luk. 19.14Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye. 12#Aro. 1.12Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; 13#Yoh. 3.5-6amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu. 14#Luk. 1.31, 35; Mat. 17.2Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
Umboni wa Yohane Mbatizi
(Mat. 3.1-12; Mrk. 1.1-8; Luk. 3.1-18)
15 # Mat. 3.11; Yoh. 8.58 Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine. 16#Aef. 1.6Chifukwa mwa kudzala kwake tinalandira ife tonse, chisomo chosinthana ndi chisomo. 17#Deut. 4.44-45; Yoh. 14.6Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu. 18#Eks. 33.20; Mat. 11.27Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.
19Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani? 20#Yoh. 3.28Ndipo anavomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Khristu. 21Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai. 22Chifukwa chake anati kwa iye, Ndiwe yani? Kuti tibwezere mau kwa iwo anatituma ife. Unena chiyani za iwe wekha? 23#Mat. 3.3Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo. 24Ndipo otumidwawo anali a kwa Afarisi. 25Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo? 26#Mat. 3.11; Yoh. 1.15Yohane anawayankha, nati, Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa, 27#Mat. 3.11; Yoh. 1.15ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira chingwe cha nsapato yake. 28Zinthu izi zinachitika mu Betaniya tsidya lija la Yordani, pomwe analikubatiza Yohane.
29 # Yes. 53.7; Yoh. 1.36; Mac. 8.32; Agal. 1.4 M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi! 30#Yoh. 15.27Ndiye amene ndinati za Iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine. 31#Mat. 3.6Ndipo sindinamdziwe Iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israele, chifukwa cha ichi ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi. 32#Mat. 3.16Ndipo Yohane anachita umboni, nati, Ndinaona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa Iye. 33#Mat. 3.11; Mac. 2.1-4Ndipo sindinamdziwe Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera. 34Ndipo ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.
Ophunzira oyamba a Yesu
35M'mawa mwakenso analikuimirira Yohane ndi awiri a ophunzira ake; 36#Yes. 53.7; Yoh. 1.36; Mac. 8.32ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu! 37Ndipo ophunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu. 38Koma Yesu anacheuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna chiyani? Ndipo anati kwa Iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti? 39Nanena nao, Tiyeni, mukaone. Pamenepo anadza naona kumene anakhala; nakhala ndi Iye tsiku lomwelo; panali monga ora lakhumi. 40Andrea mbale wake wa Simoni Petro anali mmodzi wa awiriwo, anamva Yohane, namtsata Iye. 41Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu). 42#Mat. 16.17-18Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).
43M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine. 44Koma Filipo anali wa ku Betsaida, mzinda wa Andrea ndi Petro. 45#Deut. 18.18; Yes. 9.6Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete. 46#Yoh. 7.41-42, 52Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone. 47Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo! 48Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe. 49#Mat. 14.33; 21.5Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele. 50Yesu anayankha nati kwa iye, Chifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? Udzaona zoposa izi. 51#Luk. 22.43; Mac. 1.10-11Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mudzaona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa Munthu.

Currently Selected:

YOHANE 1: BLP-2018

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy