1
Yesaya 51:12
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Yehova akuti, “Ndinetu amene ndimakutonthozani mtima. Chifukwa chiyani mukuopa munthu woti adzafa? Mukuopa munthu woti monga udzu sadzakhalitsa.
Compare
Explore Yesaya 51:12
2
Yesaya 51:16
Ndayika mawu anga mʼkamwa mwanu ndipo ndakuphimbani ndi mthunzi wa dzanja langa. Ine ndimayika pa malo pake zinthu za mlengalenga, ndipo ndinayika maziko a dziko lapansi, ndimawuza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ”
Explore Yesaya 51:16
3
Yesaya 51:7
“Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi, anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu; musaope kudzudzulidwa ndi anthu kapena kuopsezedwa akamakulalatirani.
Explore Yesaya 51:7
4
Yesaya 51:3
Yehova adzatonthozadi Ziyoni, ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse; Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni, malo ake owuma ngati munda wa Yehova. Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda ndi kundiyamika.
Explore Yesaya 51:3
5
Yesaya 51:11
Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera nakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa; chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe, chisoni ndi kubuwula zidzathawa.
Explore Yesaya 51:11